1 Israyeli ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinacurukira zipatso zace, momwemo anacurukitsa maguwa a nsembe ace; monga mwa kukoma kwace kwa dziko lace anapanga zoimiritsa zokoma.
2 Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka oparamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.
3 Pakuti tsopano adzati, Tiribe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzaticitira ciani?
4 Anena mau akulumbira monama, pakucita mapangano momwemo; ciweruzo ciphuka ngati zitsamba zowawa m'micera ya munda.
5 Okhala m'Samariya adzaopera cifanizo ca ana a ng'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ace adzamva naco cisoni, ndi ansembe ace amene anakondwera naco, cifukwa ca ulemerero wace, popeza unacicokera.
6 Adzacitengeranso ku Asuri cikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efraimu adzatenga manyazi, ndi Israyeli adzacita manyazi ndi uphungu wace.
7 Ndipo Samariya, mfumu yace yamwelera ngati thobvu pamadzi.
8 Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo cimo la Israyeli, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni.
9 Israyeli, wacimwa kuyambira masiku a Gibeya; pomwepo anaimabe; nkhondo ya pa ana a cosalungama siinawapeza ku Gibeya.
10 Pamene ndifuna ndidzawalanga, ndi mitundu ya anthu idzawasonkhanira pomangidwa iwo pa zolakwa zao ziwiri.
11 Ndipo Efraimu ndiye ng'ombe yaikazi yaing'ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lace lokoma; ndidzamsenzetsa Efraimu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya cibuluma cace.
12 Mudzibzalire m'cilungamo mukolole monga mwa cifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, nabvumbitsira inu cilungamo.
13 Mwalima coipa, mwakolola cosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakati watama njira yako ndi kucuruka kwa anthu ako amphamvu.
14 Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribeli; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ace.
15 Momwemo adzakucitirani Betele, cifukwa ca coipa canu cacikuru; mbanda kuca mfumu ya Israyeli idzalikhika konse.