Hoseya 4 BL92

Mlandu pakati pa Mulungu ndi Israyeli

1 Imvani mau a Yehova, inu ana a Israyeli; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe coonadi, kapena cifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.

2 Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kucita cigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.

3 Cifukwa cace dziko lidzacita cisoni, ndi ali yense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzacotsedwa.

4 Koma munthu asatsutsane ndi mnzace, kapena kudzudzula mnzace; popeza anthu ako ndiwo akunga otsutsana ndi wansembe.

5 Ndipo udzakhumudwa usana, ndi mneneri yemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako.

6 Anthu anga aonongeka cifukwa ca kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala cilamulo ca Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.

7 Monga anacuruka, momwemo anandicimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.

8 Adyerera cimo la anthu anga, nakhumbira cosalungama cao, yense ndi mtima wace.

9 Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga cifukwa canjira zao, ndi kuwabwezera macitidwe ao.

10 Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzacita cigololo, koma osacuruka; pakuti waleka kusamalira Yehova.

11 Cigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zicotsa mtima,

12 Anthu anga afunsira ku mtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wacigololo wawalakwitsa, ndipo acita cigololo kucokera Mulungu wao.

13 Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi miniali, ndi mkundi; popeza mthunzi wace ndi wabwino, cifukwa cace ana anu akazi acita citole, ndi apongozi anu acita cigololo.

14 Sindidzalanga ana anu akazi pocita citole iwo, kapena apongozi anu pocita cigololo iwo; pakuti iwo okha apambukira padera ndi akazi acitole, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa kucitole; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa camutu.

15 Cinkana iwe, Israyeli, ucita citole, koma asaparamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.

16 Pakuti Israyeli wacita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwana wa nkhosa ku thengo lalikuru.

17 Efraimu waphatikana ndi mafano, mlekeni.

18 Cakumwa cao casasa, acita citole kosalekeza; akuru ao akonda manyazi kwambiri.

19 Mphepo yamkulunga m'mapiko ace, ndipo adzacita manyazi cifukwa ca nsembe zao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14