1 Nenani kwa abale anu, Anthu anga, ndi kwa alongo anu, Wocitidwa-cifundo.
2 Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindiri mwamuna wace; ndipo acotse zadama zace pankhope pace, ndi zigololo zace pakati pa maere ace;
3 ndingambvule wamarisece, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati cipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;
4 ndipo ana ace sindidzawacitira cifundo; pakuti iwo ndiwo ana acigololo.
5 Pakuti mai wao anacita cigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anacita camanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine cakudya canga, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi cakumwa canga.
6 Cifukwa cace taonani, ndidzacinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ace.
7 Ndipo adzatsata omkonda koma osawakumika, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano.
8 Pakuti sanadziwa kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumcurukitsira siliva ndi golidi, zimene anapanga nazo Baala.
9 Cifukwa cace ndidzabwera ndi kucotsa tirigu wanga m'nyengo yace, ndi vinyo wanga m'nthawi yace yoikika, ndi kukwatula ubweya wanga ndi thonje langi, zimene zikadapfunda umarisece wace.
10 Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ace pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa.
11 Ndidzaleketsanso kusekerera kwace konse, madyerero ace, pokhala mwezi pace, ndi masabata ace, ndi masonkhano ace onse oikika.
12 Ndipo ndidzapasula mipesa yace ndi mikuyu yace, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.
13 Ndipo ndidzamlanga cifukwa ca masiku a Abaala amene anawafukizira, nabvala mphete za m'mphuno, ndi zokometsera zace, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova.
14 Cifukwa cace taonani, ndidzamkopa ndi kumka naye kucipululu, ndi kulankhula naye momkonda mtima.
15 Ndipo ndidzampatsa minda yace yamphesa kuyambira pomwepo, ndi cigwa ca Akori cikhale khomo la ciyembekezo; ndipo adzabvomereza pomwepo monga masiku a ubwana wace, ndi monga tsiku lokwera iye kuturuka m'dziko la Aigupto.
16 Ndipo kudzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, udzandicha Mwamuna wanga, osandichanso Baala wanga.
17 Pakuti ndidzacotsa maina a Abaala m'kamwa mwace; ndipo silidzakumbukikanso dzina lao.
18 Ndipo tsiku lomwelo ndidzawacitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzatyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zicoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.
19 Ndipo ndidzakutomera ukhale wanga kosatha, inde ndidzakutomera ukhale wanga m'cilungamo, ndi m'ciweruzo, ndi m'ukoma mtima, ndi m'cifundo.
20 Ndidzakutomeranso ukhale wanga mokhulupirika, ndipo udzadziwa Yehova.
21 Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ndidzabvomereza, ati Yehova, ndidzabvomereza thambo, ndi ilo lidzabvomereza dziko lapansi;
22 ndi dziko lapansi lidzabvomereza tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndi izi zidzabvomereza Yezreeli.
23 Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzacitira cifundo Wosacitidwa-cifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.