1 MAU a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli.
2 Ciyambi ca kunena kwa Yehova mwa Hoseya, Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wacigololo ndi ana acigololo; pakuti dziko latsata cigololo cokha cokha kuleka kutsata Yehova.
3 Ndipo anamuka natenga Gomeri mwana wamkazi wa Diblaimu; iye naima, nambalira mwana wamwamuna.
4 Ndipo Yehova anati kwa iye, Umuche dzina lace Yezreeli; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera cilango mwazi wa Yezreeli pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israyeli.
5 Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ndidzatyola uta wa Israyeli m'cigwa ca Yezreeli.
6 Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umuche dzina lace Wosacitidwacifundo; pakuti sindidzacitiranso cifundo nyumba ya Israyeli, kuti ndiwakhululukire konse.
7 Koma ndidzacitira cifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.
8 Ataleka tsono kuyamwitsa Wosacitidwa cifundo, anaima, nabala mwana wamwamuna.
9 Ndipo Yehova anati, Umuche dzina lace Si-anthuanga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.
10 Angakhale anatero, kuwerenga kwace kwa ana a Israyeli kudzanga mcenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.
11 Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israyeli adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkuru mmodzi, nadzakwera kucoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezreeli ndi lalikuru.