1 Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaeli kalonga wamkuru wakutumikira ana a anthu amtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi, yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.
2 Ndipo ambiri, a iwo ogona m'pfumbi lapansi adzauka, ena kumka ku moyo wosatha, ndi ena ku manyazi ndi mnyozo wosatha.
3 Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate cilungamo ngati nyenyezi ku nthawi za nthawi.
4 Koma iwe Danieli, tsekera mau awa, nukomere cizindikilo buku, mpaka nthawi ya cimariziro; ambiri adzathamanga cauko ndi cauko, ndi cidziwitso cidzacuruka.
5 Pamenepo ine Danieli ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m'mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzace m'mphepete mwa mtsinje tsidya lija.
6 Ndipo wina anati kwa munthu wobvala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Cimariziro ca zodabwiza izi cidzafika liti?
7 Ndipo ndinamva munthuyo wobvala bafuta wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, nakweza dzanja lace lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzacitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.
8 Ndinacimva ici, koma osacizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, citsiriziro ca izi nciani?
9 Ndipo anati, Pita Danieli; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa cizindikilo mpaka nthawi ya citsiriziro.
10 Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzacita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.
11 Ndipo kuyambira nthawi yoti idzacotsedwa nsembe yacikhalire, nicidzaimika conyansa cakupululutsa, adzakhalanso masiku cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.
12 Wodala iye amene ayembekeza, nafikira ku masiku cikwi cimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.
13 Koma iwe, muka mpaka cimariziro; pakuti udzapumula, nudzaima m'gawo lako masiku otsiriza.