Danieli 11 BL92

1 Ndipo ine, caka coyamba ca Dariyo Mmedi, ndinauka kumlimbikitsa ndi kumkhazikitsa.

2 Ndipo tsopano ndikufotokozera coonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Perisiya, ndi yacinai idzakhala yoletnera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwace idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Helene.

3 Ndipo idzauka mfumu yamphamvu, nidzacita ufumu ndi ulamuliro waukuru, nidzacita monga mwa cifuniro cace.

4 Ndipo pakuuka iye ufumu wace udzatyoledwa, nudzagawikira ku mphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yace akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wace anacita ufumu nao; pakuti ufumu wace udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.

Nkhondo ya pakati pa mfumu ya kumpoto ndi ya kumwera

5 Ndipo mfumu ya kumwela, ndiye wina wa akalonga ace, idzamposa mphamvu, nidzakhala nao ulamuliro; ulamuliro wace ndi ulamuliro waukuru.

6 Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwela adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lace; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lace; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija.

7 Koma apo pophukira mizu yace adzauka wina m'malo mwace, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzacita molimbana nao, nadzawalaka;

8 ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika za siliva ndi golidi adzazitenga kumka nazo ndende ku Aigupto; ndi zaka zace zidzaposa za mfumu ya kumpoto.

9 Ndipo adzalowa m'ufumu wa mfumu ya kumwela, koma adzabwera m'dziko lace lace.

10 Ndi ana ace adzacita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo akuru ocuruka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzacita nkhondo mpaka linga lace.

11 Ndi mfumu ya kumwela adzawawidwa mtima, nadzaturuka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukuru; koma unyinjiwo udzaperekedwa m'dzanja lace.

12 Ndipo ataucotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wace; ndipo adzagwetsa zikwi makumi makumi, koma sadzalakika.

13 Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wa kuposa oyamba aja; nidzafika pa cimariziro ca nthawi, ca zaka, ndi khamu lalikuru la nkhondo ndi cuma cambiri.

14 Ndipo nthawi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwela, ndi aciwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo.

15 Ndi mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda midzi yamalinga; ndi ankhondo a kumwela sadzalimbika, ngakhale anthu ace osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika.

16 Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzacita cifuniro cace ca iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pace; ndipo adzaima m'dziko lokometsetsalo, ndi m'dzanja mwace mudzakhala cionongeko.

17 Ndipo adzalimbitsa nkhope yace, kudza ndi mphamvu ya ufumu wace wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzacita cifuniro cace, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kubvomerezana naye.

18 Pambuyo pace adzatembenuzira nkhope yace kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwace adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwace.

19 Pamenepo adzatembenuzira nkhope yace ku malinga a dziko lace lace; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso.

20 Ndipo m'malo mwace adzauka wina wakupititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo; koma atatha masiku owerengeka adzatyoledwa iye, si mwamkwiyo, kapena kunkhondo ai.

21 Ndi m'malo mwace adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatsa ulemu wa ufumu, koma adzafika kacetecete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika.

22 Ndipo mwa mayendedwe ace a cigumula adzakokololedwa pamaso pace, nadzatyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa cipangano.

23 Ndipo atapangana naye adzacita monyenga; pakuti adzakwera, nadzasanduka wamphamvu ndi anthu owerengeka.

24 Adzafika kacetecete ku minda yokometsetsa ya derali, nadzacita cosacita atate ace, kapena makolo ace; adzawawazira zofunkha, ndi zankhondo, ndi cuma, nadzalingiririra malinga ziwembu zace; adzatero nthawi.

25 Nadzautsa mphamvu yace ndi mtima wace ayambane ndi mfumu ya kumwela ndi khamu lalikuru la nkhondo; ndi mfumu ya kumwela ndi khamu lalikuru ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu.

26 Inde iwo akudyako cakudya cace adzamuononga; ndi ankhondo ace adzasefukira, nadzagwaambiri ophedwa.

27 Ndipo mafumu awa onse awiri mitima yao idzakumbuka kucita zoipa, nadzanena bodza ali pa gome limodzi; koma osapindula nalo; pakuti kutha kwace kudzakhala pa nthawi yoikika.

28 Ndipo adzabwerera ku dziko lace ndi cuma cambiri; ndi mtima wace udzatsutsana ndi cipangano copatulika, nadzacita cifuniro cace, ndi kubwerera ku dziko lace.

29 Pa nthawi yoikika adzabwera, nadzalowa kumwela; koma sikudzakhala monga nthawi yoyamba ija, kapena yotsirizayi.

30 Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; cifukwa cace adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi cipangano copatulika, nadzacita cifuniro cace; adzabweranso, nadzasamalira otaya cipangano copatulika.

31 Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lace; nadzacotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa conyansa copululutsaco.

32 Ndipo akucitira coipa cipanganoco iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzacita mwamphamvu.

33 Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi lawi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri.

34 Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling'ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika.

35 Nadzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthawi ya citsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthawi yoikika.

36 Ndipo mfumu idzacita monga mwa cifuniro cace, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iri yonse nidzanena zodabwiza pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzacitidwa ukaliwo; pakuti cotsimikizika m'mtimaco cidzacitika.

37 Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ace, kapena coikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iri yonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.

38 Koma kumalo kwace idzacitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ace sanaudziwa, adzaulemekeza ndi golidi, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wace, ndi zinthu zofunika.

39 Ndipo adzacita molimbana ndi malinga olimba koposa, pomthandiza mulungu wacilendo; ali yense wombvomereza adzamcurukitsira ulemu, nadzawacititsa ufumu pa ambiri, nadzagawa dziko mwa mtengo wace.

40 Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwela idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kabvumvulu, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.

41 Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lace ndi awa: Edomu, ndi Moabu, ndi oyamba a ana a Amoni.

42 Adzatambalitsiranso dzanja lace kumaiko; dziko la Aigupto lomwe silidzapulumuka.

43 Ndipo adzacita mwamphamvu ndi cuma ca golidi, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Aigupto; Alubi ndi Akusi adzatsata mapazi ace.

44 Koma mbiri yocokera kum'mawa ndi kumpoto idzambvuta; nadzaturuka iye ndi ukali waukuru kupha ndi kuononga konse ambiri.

45 Ndipo adzamanga mahema a nyumba yacifumu yace pakati pa nyanja yamcere ndi phiri lopatulika lofunika; koma adzafikira cimariziro cace wopanda wina wakumthandiza.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12