Danieli 8 BL92

Masomphenya a nkhosa yamphongo ndi tonde

1 Caka cacitatu ca Belisazara mfumu masomphenya anandionekera kwa ine Danieli, atatha kundionekera oyamba aja.

2 Ndipo ndinaona m'masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali m'Susani, m'nyumba ya mfumu, ndiwo m'dziko la Elamu; ndinaona m'masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai.

3 Ndipo ndinakweza maso anga ndi kupenya; taonani, panaima pamtsinje nkhosa yamphongo yokhala nazo nyanga ziwiri, ndi nyanga ziwirizo zinali za msinkhu wautali, koma imodzi inaposa inzace; yoposayo inaphuka m'mbuyo.

4 Ndinaona nkhosa yamphongo irikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwela; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pace; panalibenso wakulanditsa m'dzanja lace; koma inacita monga mwa cifuniro cace, nidzikulitsa.

5 Ndipo polingirfrapo ine, taonani, wadza tonde wocokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pa maso ace.

6 Ndipo anadzera nkhosa yamphongoyo yokhala ndi nyanga ziwiri, imene ndidaiona irikuima kumtsinje, naithamangira ndi mphamvu yace yaukali.

7 Ndipo ndinamuona wayandikira pafupi pa nkhosa yamphongo, nawawidwa mtima nayo, naigunda nkhosa yamphongo, natyola nyanga zace ziwiri; ndipo mphongoyo inalibe mphamvu yakuima pamaso pace, koma anaigwetsa pansi, naipondereza; ndipo panalibe wakupulumutsa mphongoyo m'dzanja lace.

8 Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukuru, koma atakhala wamphamvu, nyanga yace yaikuru inatyoka; ndi m'malo mwace munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza ku mphepo zinai za mlengalenga.

9 Ndipo mu imodzi ra izi munaphuka nyanga yaing'ono, imene inakula kwakukuru ndithu, kuloza kumwela, ndi kum'mawa, ndi ku dziko lokometsetsa.

10 Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, nizipondereza.

11 Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimcotsera nsembe yopsereza yacikhalire; ndi pokhala malo ace opatulika panagwetsedwa.

12 Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yacikhalire mwa kulakwa kwace, nigwetsa pansi coonadi, nicita cifuniro cace, nikuzika.

13 Pamenepo ndinamva wina woyera, alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yacikhalire, ndi colakwa cakupululutsa ca kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti?

14 Nati kwa ine, Mpaka masiku zikwi ziwiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama.

15 Ndipo kunali, nditaona masomphenyawo, ine Danieli ndinafuna kuwazindikira; ndipo taonani, panaima popenyana ndi ine ngati maonekedwe a munthu.

16 Ndipo ndinamva mau a munthu pakati pa magombe a Ulai, naitana, nati, Gabrieli, zindikiritsa munthuyu masomphenyawo.

17 Nayandikira iye poima inepo; atadza iye tsono ndinacita mantha, ndinagwa nkhope pansi; koma anati kwa ine, Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthawi ya cimariziro.

18 Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikuru, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo,

19 Ndipo anati, Taona, ndidzakudziwitsa cimene cidzacitika pa citsiriziro ca mkwiyowo; pakuti pa nthawi yoikika mpakutha pace,

20 Nkhosa yamphongo waiona ya nyanga ziwiri ndizo mafumu a Mediya ndi Perisiya.

21 Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Helene, ndi nyanga yaikuru iri pakati pa maso ace ndiyo mfumu yoyamba.

22 Ndi kuti zinaphuka zinai m'malo mwace mwa iyo itatyoka, adzauka maufumu anai ocokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja.

23 Ndipo potsiriza pace pa ufumu wao, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi.

24 Ndi mphamvu yace idzakhala yaikuru, koma si mphamvu yace yace ai, nidzaononga modabwiza, nidzakuzika, ndi kucita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo.

25 Ndipo mwa kucenjera kwace adzapindulitsa cinyengo m'dzanja mwace, nadzadzikuza m'mtima mwace; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzatyoledwa popanda dzanja.

26 Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzacitika atapita masiku ambiri.

27 Ndipo ine Danieli ndinakomoka ndi kudwala masiku ena; pamenepo ndinauka ndi kucita nchito ya mfumu; ndipo ndinadabwa nao masomphenyawo, koma panalibe wakuwazindikiritsa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12