Danieli 5 BL92

Madyerero a Belisazara, dzanja lolemba pakhoma

1 Mfumu Belisazara anakonzera anthu ace akulu cikwi cimodzi madyerero akuru, namwa vinyo pamaso pa cikwico.

2 Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golidi ndi siliva adazicotsa Nebukadinezara atate wace ku Kacisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akuru ace, akazi ace ndi akazi ace ang'ono, amweremo.

3 Nabwera nazo zotengera zagolidi adazicotsa ku Kacisi wa nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo mfumu ndi akuru ace, akazi ace ndi akazi ace ang'ono, anamweramo.

4 Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolidi, ndi yasiliva, yamkuwa, yacitsulo, yamtengo, ndi yamwala.

5 Nthawi yomweyo zinabuka zala za dzanja la munthu, nizinalemba pandunji pa coikapo nyali, pomata pa khoma la cinyumba ca mfumu; ndipo mfumu inaona nsonga yace ya dzanja lidalembalo.

6 Pamenepo padasandulika pa nkhope pace pa mfumu, ndi maganizo ace anamsautsa, ndi mfundo za m'cuuno mwace zinaguruka, ndi maondo ace anaombana.

7 Nipfuulitsa mfumu abwere nao openda, Akasidi, ndi alauli, Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babulo, Ali yense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwace, adzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwace, nadzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwu.

8 Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoza kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwace.

9 Ndipo mfumu Belisazara anabvutika kwambiri, ndi nkhope yace inasandulika, ndi akuru ace anathedwa nzeru.

10 Cifukwa ca mau a mfumu ndi akuru ace mkazi wamkuru wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakubvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike;

11 pali munthu m'ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkuru wa alembi, openda, Akasidi, ndi alauli;

12 popeza m'Danieli yemweyo, amene mfumu adamucha Belitsazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi cidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa, ndi kumasula mfundo. Amuitane Danieli tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.

Danieli amasulira lemba lolembedwa pakhoma

13 Pamenepo analowa naye Danieli kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Danieli, Ndiwe kodi Danieli uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda?

14 Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana.

15 Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace; koma sanakhoza kufotokozera kumasulira kwa cinthuci.

16 Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace, udzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwo.

17 Pamenepo anayankha Danieli, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwace.

18 Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi cifumu;

19 ndipo cifukwa ca ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, a manenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pace; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.

20 Koma pokwezeka mtima wace, nulimba mzimu wace kucita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wace, namcotsera ulemerero wace;

21 ndipo anamuinga kumcotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wace unasandulika ngati wa nyama za kuthengo, ndi pokhala pace mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lace linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, nauikira ali yense Iye afuna mwini.

22 Ndipo inu mwana wace, Belisazara inu, simunadzicepetsa m'mtima mwanu, cinkana munazidziwa izi zonse;

23 koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yace kwa inu; ndi inu ndi akuru anu, akazi anu ndi akazi anu ang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolidi, yamkuwa, yacitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona, kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwace muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamcitira ulemu.

24 Pamenepo nsonga ya dzanja inatumidwa kucokera pamaso pace, nililembedwa lembali.

25 Ndipolembalolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL UF ARSIN.

26 Kumasulira kwace kwa mau awa ndi uku: MENE, Mulungu anawerenga ufumu wanu, nautha.

27 TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera.

28 PERES, ufumu wanu wagawika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.

29 Pamenepo Belisazara analamulira, ndipo anabveka Danieli cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwace, nalalikira za iye kuti ndiye wolamulira wacitatu m'ufumumo.

30 Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa.

31 Ndipo Dariyo Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12