1 Caka coyamba ca Belisazara mfumu ya ku Babulo Danieli anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwace pakama pace; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwacidule.
2 Danieli ananena, nati, Ndinaona m'masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikuru.
3 Ndipo zinaturuka m'nyanja zirombo zazikuru zinai zosiyana-siyana.
4 Coyamba cinanga mkango, cinali nao mapiko a ciombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zace zinathothoka, nicinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, nicinapatsidwa mtima wa munthu.
5 Ndipo taonani, cirombo cina caciwiri cikunga cimbalangondo cinatundumuka mbali imodzi; ndi m'kamwa mwace munali nthiti zitatu pakati pa mano ace; ndipo anatero naco, Nyamuka, lusira nyama zambiri.
6 Pambuyo pace ndinapenya ndi kuona cina ngati nyalugwe, cinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pace, ciromboco cinali nayonso mitu inai, nicinapatsidwa ulamuliro.
7 Pambuyo pace ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona cirombo cacinai, coopsa ndi cocititsa mantha, ndi camphamvu coposa, cinali nao mano akuru acitsulo, cinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza cotsala ndi mapazi ace; cinasiyana ndi zirombo zonse zidacitsogolera; ndipo cinali ndi nyanga khumi.
8 Ndinali kulingirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga yina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pace zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikuru.
9 Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yacifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zobvala zace zinali za mbu ngati cipale cofewa, ndi tsitsi la pa mutu pace ngati ubweya woyera, mpando wacifumu unali malawi amoto, ndi njinga zace moto woyaka.
10 Mtsinje wamoto unayenda woturuka pamaso pace, zikwi zikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pace, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.
11 Pamenepo ndinapenyera cifukwa ca phokoso la mau akuru idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adacipha ciromboci, ndi kuononga mtembo wace, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto.
12 Ndipo zirombo zotsalazo anazicotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhalenso nyengo ndi nthawi.
13 Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pace.
14 Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wace ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wace sudzaonongeka.
15 Koma ine Danieli, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandibvuta.
16 Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za coonadi za ici conse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwace kwa zinthuzi:
17 Zirombo zazikuru izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi.
18 Koma opatulika la Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, ku nthawi zomka muyaya.
19 Pamenepo ndinafuna kudziwa coonadi ca cirombo cacinai cija cidasiyana nazo zonsezi, coopsa copambana, mano ace acitsulo, ndi makadabo ace amkuwa, cimene cidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ace;
20 ndi za nyanga khumi zinali pamutu pace, ndi nyanga yina Idaphukayi, imene zidagwa zitatu patsogolo pace; nyangayo idali ndi maso ndi pakamwa pakunena zazikuru, imene maonekedwe ace anaposa zinzace.
21 Ndinapenya, ndipo nyanga yomweyi inacita nkhondo ndi opatulikawo, niwalaka, mpaka inadza Nkhalamba ya kale lomwe;
22 ndi mlandu unakomera opatulika a Wam'mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo.
23 Anatero, cirombo cacinai ndico ufumu wacinai pa dziko lapansi, umene udzasiyana nao maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya.
24 Kunena za nyanga khumi, m'ufumu uwu adzauka mafumu khumi, ndi pambuyo pao idzauka yina; iyo idzasiyana ndi oyamba aja, nidzacepetsa mafumu atatu.
25 Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambainwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi cilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lace mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.
26 Koma woweruza mlandu adzakhalako, ndipo adzacotsa ulamuliro wace, kuutha ndi kuuononga kufikira cimariziro.
27 Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu a opatulika a Wam'mwambamwamba; ufumu wace ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzamtumikira ndi kummvera.
28 Kutha kwace kwa cinthuci nkuno. Ine Danieli, maganizo anga anandibvuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga cinthuci m'mtima mwanga.