1 Kudamkomera Dariyo kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m'madera onse a ufumu;
2 ndi akuyang'anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Danieli; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke.
3 Pamenepo Danieli amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang'anira ufumu wonse.
4 Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola cifukwa Danieli, kunena za ufumuwo; koma sanakhoza kupeza cifukwa kapena colakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo sanaona cosasamala kapena colakwa ciri conse mwa iye.
5 Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola cifukwa ciri conse Danieli amene, tikapanda kumtola ici pa cilamulo ca Mulungu wace.
6 Ndipo akuru awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo cikhalire.
7 Akuru onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lacifumu, ndi kuikapo coletsa colimba, kuti ali yense akapempha kanthu kwa mulungu ali yense, kapena kwa munthu ali yense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango,
8 Tsopano, mfumu, mukhazikitse coletsaco, ndi kutsimikiza colembedwaco, kuti cisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika.
9 Momwemo mfumu Dariyo anatsimikiza colembedwa ndi coletsaco.
10 Ndipo podziwa Danieli kuti adatsimikiza colembedwaco, analowa m'nyumba mwace, m'cipinda mwace, cimene mazenera ace anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwadamaondo ace tsiku limodzi katatu, napemphera, nabvomereza pamaso pa Mulungu wace monga umo amacitira kale lonse.
11 Pamenepo anasonkhana anthu awa, napeza Danieli alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wace.
12 Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za coletsaco ca mfumu, Kodi simunatsimikiza coletsaco, kuti ali yense akapempha kanthu kwa mulungu ali yense, kapena kwa munthu ali yense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Coona cinthuci, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.
13 Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Danieli uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena coletsa munacitsimikizaco; koma apempha pemphero lace katatu tsiku limodzi.
14 Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wace pa Danieli kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.
15 Koma anthu awa anasonkhana kwa mfumu, nati kwa mfumu, Dziwani, mfumu, kuti lamulo la Amedi ndi Aperisi, ndilo kuti coletsa ciri conse ndi lemba liri lonse idazikhazikira mfumu, zisasinthike.
16 Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Danieli, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Danieli, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.
17 Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi cosindikizira cace, ndi cosindikizira ca akuru ace, kuti kasasinthike kanthu ka Danieli.
18 Pamenepo mfumu inamuka ku cinyumba cace, nicezera kusala usikuwo, ngakhale zoyimbitsa sanabwera nazo pamaso pace, ndi m'maso mwace munamuumira.
19 Nilawira mamawa mfumu, nimuka mofulumira ku dzenje la mikango.
20 Ndipo poyandikira padzenje inapfuula ndi mau acisoni mfumu, ninena, niti kwa Danieli, Danieli, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwamikango?
21 Pamenepo Danieli anati kwa mfumu, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire.
22 Mulungu wanga watuma mthenga wace, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, cifukwa anandiona wosacimwa pamaso pace, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwa.
23 Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza aturutse Danieli m'dzenje. Momwemo anamturutsa Danieli m'dzenje, ndi pathupi pace sipadaoneka bala, popeza anakhulupirira Mulungu wace.
24 Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Danieli, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.
25 Pamenepo mfumu Dariyo analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala pa dziko lonse lapansi, Mtendere ucurukire inu.
26 Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Danieli; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala cikhalire, ndi ufumu wace ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwace kudzakhala mpaka cimariziro.
27 Iye apulumutsa, nalanditsa, nacita zizindikilo ndi zozizwa m'mwamba ndi pa dziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Danieli ku mphamvu ya mikango.
28 Momwemo Danieli amene anakuzikabe pokhala Dariyo mfumu, ndi pokhala mfumu Koresi wa ku Perisiya.