Danieli 1 BL92

Maleredwe a Danieli ndi anzace kwa mfumu ya ku Babulo

1 CAKA cacitatu ca Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo adadza ku Yerusalemu, naumangira misasa ya nkhondo.

2 Ndipo Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lace, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye ku dziko la Sinara, ku nyumba ya mulungu wace, nalonga zipangizozo m'nyumba ya cuma ca mulungu wace.

3 Ndipo mfumu inauza Asipenazi mkuru wa adindo kuti abwere nao ena a ana a Israyeli, a mbeu ya mafumu, ndi ya akalonga;

4 anyamata opanda cirema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ocenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'cinyumba ca mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Akasidi.

5 Ndipo mfumu inawaikira gawo la cakudya ca mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye, ndi kuti awalere zaka zitatu, kuti potsiriza pace aimirire pamaso pa mfumu.

6 Mwa awa tsono munali a ana a Yuda, Danieli, Hananiya, Misayeli, ndi Azariya.

7 Ndi mkuru wa adindo anawapatsa maina ena; Danieli anamucha Belitsazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaeli, Mesaki; ndi Azariya, Abedinego.

8 Koma Danieli anatsimikiza mtimti kuti asadzidetse ndi cakudya ca mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; cifukwa cace anapempha mkuru wa adindo amlole asadzidetse.

9 Ndipo Mulungu anamkometsera Danieli mtima wa mkuru wa adindo, amcitire cifundo.

10 Nati mkuru wa adindo kwa Danieli. Ine ndiopa mbuyanga mfumu, amene anakuikirani cakudya canu ndi cakumwa canu; pakuti aonerenji nkhope zanu zacisoni zoposa za anyamata olingana ndi inu? momwemo mudzaparamulitsa mutu wanga kwa mfumu.

11 Nati Danieli kwa kapitao, amene mkuru wa adindo adamuikayo ayang'anire Danieli, Hananiya, Misaeli, ndi Azariya,

12 Muyesetu anyamata anu masiku khumi; atipatse zomera m'nthaka tidye, ndi madzi timwe.

13 Pamenepo mupenye maonekedwe athu ndi maonekedwe a anyamata akudya cakudya ca mfumu; ndi monga umo muonera, mucitire anyamata anu.

14 Ndipo anawamvera mau awa, nawayesa masiku khumi.

15 Atatha masiku khumiwo tsono, anaona kuti maonekedwe ao ndi kunenepa kwao anaposa anyamata onse adadyawo zakudya za mfumu.

16 Pamenepo kapitaoyo anacotsa cakudya cao ndi vinyo akadamwa, nawapatsa zomera m'nthaka.

17 Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa cidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Danieli anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.

18 Atatha masiku inanenawo mfumu kuti alowe nao, mkulu wa adindo analowa nao pamaso pa Nebukadinezara.

19 Ndipo mfumu inalankhula nao, koma mwa iwo onse sanapezeka monga Danieli, Hananiya, Misaeli, ndi Azariya; naimirira iwo pamaso pa mfumu.

20 Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira, inawapeza akuposa alembi ndi openda onse m'ufumu wace wonse.

21 Nakhala moyo Danieli mpaka caka coyamba ca Koresi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12