Danieli 4 BL92

Loto la Nebukadinezara la mtengo waukuru

1 Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe okhala pa dziko lonse lapansi: Mtendere ucurukire inu.

2 Candikomera kuonetsa zizindikilo ndi zozizwa, zimene anandicitira Mulungu Wam'mwambamwamba.

3 Ha! zizindikilo zace nzazikuru, ndi zozizwa zace nza mphamvu, ufumu wace ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwace ku mibadwo mibadwo.

4 Ine Nebukadinezara ndinalimkupumula m'nyumba mwanga, ndi kukhala mwaufulu m'cinyumba canga,

5 Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingilira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandibvuta ine.

6 Cifukwa cace ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babulo, kuti andidziwitse kumasulira kwace kwa lotoli.

7 Pamenepo anafika alembi, openda, Akasidi, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitsa kumasulira kwace.

8 Koma potsiriza pace analowa pamaso panga Danieli, dzina lace ndiye Belitsazara, monga mwa dzina la mulungu wanga, amenenso muli mzimu wa milungu yoyera m'mtima mwace; ndipo ndinamfotokozera lotoli pamaso pace, ndi kuti,

9 Belitsazara iwe, mkuru wa alembi, popeza ndidziwa kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera, ndi kuti palibe cinsinsi cikusautsa, undifotokozere masomphenya a loto langa ndalotali, ndi kumasulira kwace.

10 Masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga ndi awa: Ndinapenya ndi kuona mtengo pakati pa dziko lapansi, msinkhu wace ndi waukuru.

11 Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wace unafikira kumwamba, nuonekera mpaka cilekezero ca dziko lonse lapansi.

12 Masamba ace anali okoma, ndi zipatso zace zinacuruka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wace, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zace, ndi nyama zonse zinadyako.

13 Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba.

14 Anapfuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zace, yoyolani masamba ace, mwazani zipatso zace, nyama zicoke pansi pace, ndi mbalame pa nthambi zace.

15 Koma siyani citsa ndi mizu yace m'nthaka, comangidwa ndi mkombero wa citsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo; ncokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lace likhale pamodzi ndi nyama ziri m'macire a m'dziko.

16 Mtima wace usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, nizimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri.

17 Citsutso ici adacilamulira amithenga oyerawo, anacifunsa, nacinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.

18 Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitsazara, undifotokozere kumasulira kwace, popeza anzeru onse a m'ufumu wanga sakhoza kundidziwitsa kumasulira kwace; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.

Danieli ammasulira lotolo

19 Pamenepo Danieli, dzina lace ndiye Belitsazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ace. Mfumu inayankha, niti, Belitsazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwace. Belitsazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwace kwa iwo akuutsana nanu.

20 Mtengo mudauona umene unakula, nukhala wolimba, nufikira kumwamba msinkhu wace, nuonekera pa dziko lonse lapansi,

21 umene masamba ace anali okoma, ndi zipatso zace zocuruka, ndi m'menemo munali cakudya cofikira onse, umene nyama za kuthengo zinakhala pansi pace, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yace;

22 ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku cilekezero ca dziko lapansi.

23 Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani citsa cace ndi mizu m'nthaka, comangidwa ndi mkombero wa citsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo, nicikhale cokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lace likhale pamodzi ndi nyama za kuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri;

24 kumasulira kwace ndi uku, mfumu; ndipo cilamuliro ca Wam'mwambamwamba cadzera mbuye wanga mfumu:

25 kuti adzakuingitsani kukucotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna mwini.

26 Ndipo kuti anauza asiye citsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira.

27 Cifukwa cace, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani macimo anu ndi kucita cilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kucitira aumphawi cifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.

Nebukadinezara acita misala

28 Conseci cinagwera mfumu Nebukadinezara.

29 Itatha miyezi khumi ndi iwiri, analikuyenda m'cinyumba cacifumu ca ku Babulo.

30 Mfumu inanena, niti, Suyu Babulo wamkuru ndinammanga, akhale pokhala pacifumu, ndi mphamvu yanga yaikuru uoneke ulemerero wa cifumu canga?

31 Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ocokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakucokera.

32 Nadzakuinga kukucotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; nizidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna mwini.

33 Nthawi yomweyo anacitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumcotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng'ombe iye, ndi thupi lace linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lace lidamera ngati nthenga za ciombankhanga ndi makadabo ace ngati makadabo a mbalame.

34 Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumcitira ulemu Iye wokhala cikhalire; pakuti kulamulira kwace ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wace ku mibadwo mibadwo;

35 ndi okhala pa dziko lapansi onse ayesedwa acabe; ndipo Iye acita mwa cifunito cace m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lace, kapena wakunena naye, Mucitanji?

36 Nthawi yomweyi nzeru zanga zinandibwerera, ndi cifumu canga ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uonekenso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akuru anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika m'ufumu wanga, Iye nandioniezeranso ukulu wocuruka.

37 Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti nchito zace zonse nzoona, ndi njira zace ciweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwacepetsa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12