1 Caka cacitatu ca Koresi mfumu ya Perisiya, cinabvumbulutsidwa cinthu kwa Danieli, amene anamucha Belitsazara; ndipo cinthuco ncoona, ndico nkhondo yaikuru; ndipo anazindikira cinthuco, nadziwa masomphenyawo.
2 Masiku aja ine Danieli ndinali kulira masabata atatu amphumphu,
3 Cakudya cofunika osacidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu,
4 Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi woyamba, pokhala ine m'mphepete mwa mtsinje waukuru, ndiwo Hidikeli,
5 ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wobvala bafuta, womanga m'cuuno ndi golidi woona wa ku Ufazi;
6 thupi lace lomwe linanga berulo, ndi nkhope yace ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ace ngati nyali zamoto, ndi manja ace ndi mapazi ace akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ace kunanga phokoso la aunyinji.
7 Ndipo ine Danieli ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaona masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukuru, nathawa kubisala.
8 Momwemo ndinatsala ndekha, ndipo ndinaona masomphenya akuruwa, koma wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukoma kwanga kunasandulika cibvundi mwa ine, wosakhalanso ndi mphamvu ine.
9 Ndipo ndinamva kunena kwa mau ace, ndipo pamene ndinamva kunena kwa mau ace ndinagwidwa ndi tulo tatikuru pankhope panga, nkhope yanga pansi.
10 Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga.
11 Nati kwa ine, Danieli, munthu wokondedwatu iwe, tazindikira mau ndirikunena ndi iwe, nukhale ciriri; pakuti ndatumidwa kwa iwe tsopano. Ndipo pamene adanena mau awa kwa ine ndinaimirira ndi kunjenjemera.
12 Pamenepo anati kwa ine, Usaope Danieli; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzicepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako,
13 Koma kalonga wa ufumu wa Perisiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaeli, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Perisiya.
14 Ndadzera tsono kukuzindikiritsa codzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo.
15 Ndipo atanena ndi ine monga mwa mau awa, ndinaweramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala du.
16 Ndipo taonani, wina wakunga ana a anthu anakhudza milomo yanga; pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndi kunena naye woima popenyana nane, Mbuye wanga, cifukwa ca masomphenyawo zowawa zanga zandibwerera, ndipo ndiribenso mphamvu.
17 Pakuti mnyamata wa mbuye wanga inu akhoza bwanji kulankhula ndi mbuye wanga inu? pakuti ine tsopano apa mulibenso mphamvu mwa ine, osanditsaliranso mpweya.
18 Pamenepo anandikhudzanso wina, maonekedwe ace ngati munthu, nandilimbikitsa ine.
19 Nati, Munthu wokondedwatu iwe, Usaope, mtendere ukhale nawe; limbika, etu limbika. Ndipo pamene ananena ndi ine ndinalimbikitsidwa, ndinati, Anene mbuye wanga; pakuti mwandilimbikitsa.
20 Pamenepo anati, Kodi udziwa cifukwa coti ndakudzera? ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Perisiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Helene.
21 Koma ndidzakufotokozera colembedwa pa lemba la coonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaeli kalonga wanu.