Danieli 2 BL92

Nebukadinezara alota, Danieli ammasulira lotolo

1 Caka caciwiri ca Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wace unabvutika, ndi tulo tace tidamwazikira.

2 Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Akasidi, amuululire mfumu maloto ace. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu.

3 Niti nao mfumu, Ndalota loto, nubvutika mzimu wanga kudziwa lotolo.

4 Pamenepo Akasidi anati kwa mfumu m'Ciaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwace.

5 Niyankha mfumu, niti kwa Akasidi, Candicokera cinthuci; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lace, mudzadulidwa nthuli nthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala.

6 Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwace, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukuru; cifukwa cace mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwace.

7 Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ace lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwace.

8 Mfumu inayankha, niti, Ndidziwatu kuti mukunkhuniza dala, pakuona inu kuti cinthuci candicokera.

9 Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; cifukwa cace mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwace komwe.

10 Akasidi anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu pa dziko lapansi wokhoza kuulula mlandu wa mfumu; cifukwa cace palibe mfumu, mkuru, kapena wolamulira, wafunsira cinthu cotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Akasidi ali onse.

11 Pakuti cinthu acifuna mfumu ncapatali; ndipo palibe wina wokhoza kuciulula pamaso pa mfumu, koma milungu imene kwao sikuli pamodzi ndi anthu.

12 Cifukwa cace mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse m'Babulo.

13 M'mwemo cilamuliroco cidamveka, ndi eni nzeru adati aphedwe; anafuna-funanso Danieli ndi anzace aphedwe.

14 Pamenepo Danieli anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Arioki mkuru wa olindirira a mfumu, adaturukawo kukapha eni nzeru a ku Babulo;

15 anayankha nati kwa Arioki mkuru wa olindirira a mfumu, Cilamuliro ca mfumu cifulumiriranji? Pamenepo Arioki anadziwitsa Danieli cinthuci.

16 Nalowa Danieli, nafunsa mfumu amuikire nthawi, kuti aululire mfumu kumasulira kwace.

17 Pamenepo Danieli anapita ku nyumba kwace, nadziwitsa anzace Hananiya, Misaeli, ndi Azariya, cinthuci;

18 kuti apemphe zacifundo kwa Mulungu wa Kumwamba pa cinsinsi ici; kuti Danieli ndi anzace asaonongeke pamodzi ndi eni nzeru ena a ku Babulo.

19 Pamenepo cinsinsico cinabvumbulutsidwa kwa Danieli m'masomphenya a usiku. Ndipo Danieli analemekeza Mulungu wa Kumwamba.

20 Danieli anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi, a pakuti nzeru ndi mphamvu ziri zace;

21 pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, acotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi cidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.

22 Iye abvumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.

23 Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ici tacifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.

24 Potero Danieli analowa kwa Arioki amene mfumu idamuika aononge eni nzeru a ku Babulo; anamuka, natero naye, Usaononga eni nzeru a ku Babulo, undilowetse kwa mfumu, ndipo ndidzaululira mfumu kumasulirako.

25 Pamenepo Arioki analowa naye Danieli kwa mfumu mofulumira; natero nayo, Ndapeza munthu wa ana a ndende a Yuda, ndiye adzadziwitsa mfumu kumasulira kuja.

26 Mfumu inayankha, niti kwa Danieli, amene dzina lace ndiye Belitsazara, Ukhoza kodi kundidziwitsa lotolo ndidalilota, ndi kumasulira kwace?

27 Nayankha Danieli pamaso pa mfumu, nati, Cinsinsi inacitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sakhoza kuciululira mfumu;

28 koma kuli Mulungu Kumwamba wakubvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara cimene cidzacitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m'mtima mwanu pakama panu, ndi awa:

29 Inu mfumu, maganizo anu analowa m'mtima mwanu muli pakama panu, akunena za ico cidzacitika m'tsogolomo; ndipo Iye amene abvumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani codzacitikaco.

30 Koma ine, cinsinsi ici sicinabvumbulutsidwa kwa ine cifukwa ca nzeru ndiri nayo yakuposa wina ali yense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.

31 Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikuru. Fanoli linali lalikuru, ndi kunyezimira kwace kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ace anali oopsa,

32 Pano ili tsono, mutu wace unali wagolidi wabwino, cifuwa cace ndi manja ace zasiliva, mimba yace ndi cuuno cace zamkuwa,

33 miyendo yace yacitsulo, mapazi ace mwina citsulo mwina dongo.

34 Munali cipenyere kufikira mwala unasemedwa popanda manja, umene unagunda fanoli pa mapazi ace okhala citsulo ndi dongo, nuwaphwanya.

35 Pamenepo citsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golidi, zinapereka pamodzi, nizinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikuru, nudzaza dziko lonse lapansi.

36 Ili ndi loto; kumasulira kwace tsono tikufotokozerani mfumu.

37 Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wa Kumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikuru, ndi ulemu;

38 ndipo pali ponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakucititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolidi.

39 Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wocepa ndi wanu, ndi ufumu wina wacitatu wamkuwa wakucita ufumu pa dziko lonse lapansi.

40 Ndi ufumu wacinai udzakhala wolimba ngati citsulo, popeza citsulo ciphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga citsulo ciswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa.

41 Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zace, mwina dongo la woumba, mwina citsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya citsulo; popeza mudaona citsulo cosanganizika ndi dongo.

42 Ndi zala za mapazi, mwina citsulo ndi mwina dongo, momwemo ufumuwo, mwina wolimba mwina wogamphuka.

43 Ndi umo mudaonera citsulo cosanganizika ndi dongo, iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma sadzapharikizana, monga umo citsulo sicimasanganizikana ndi dongo.

44 Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzao nongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wace sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse nudzakhala cikhalire.

45 Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera citsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golidi; Mulungu wamkuru wadziwitsa mfumu cidzacitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwace kwakhazikika.

46 Pamenepo mfumu Nebukadinezara anagwa nkhope yace pansi, nalambira Danieli, nati amthirire nsembe yaufa ndi ya zonunkhira zokoma.

47 Mfumu inamyankha Danieli, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wobvumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kubvumbulutsa cinsinsi ici.

48 Pamenepo mfumu inasandutsa Danieli wamkuru, nimpatsa mphatso zazikuru zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babulo; nakhala iye kazembe wamkuru wa anzeru onse a ku Babulo.

49 Pamenepo Danieli anapempha mfumu, ndipo anaika Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, ayang'anire nchito za dera la ku Babulo. Koma Danieli anakhala m'bwalo la mfumu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12