1 Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Heteloni, polowera ku Hamati, Hazarenani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zace zilinge kum'mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi.
2 Ndi m'malire a Dani, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Aseri, limodzi.
3 Ndi m'malire a Aseri, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Nafitali, limodzi.
4 Ndi m'malire a Nafitali, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Manase, limodzi.
5 Ndi m'malire a Manase, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Efraimu, limodzi.
6 Ndi m'malire a Efraimu, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Rubeni, limodzi.
7 Ndi m'malire a Rubeni, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Yuda, limodzi.
8 Ndi m'malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale copereka a mucipereke, mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwace, ndi m'litali mwace lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pace.
9 Copereka mucipereke kwa Yehova cikhale ca mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace.
10 Ndipo m'mwemo mudzakhala copereka copatulika ca ansembe kumpoto, zikwi makumi awiri mphambu zisanu a m'litali mwace, ndi kumadzulo zikwi khumi kupingasa kwace, ndi kum'mawa zikwi khumi kupingasa kwace, ndi kumwela zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace; ndi pakati pace pakhale malo opatulika a Yehova.
11 Cidzakhala ca ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israyeli, ndi muja anasokera Alevi.
12 Ndi ciperekoco cikhale cao cotapa pa copereka ca dziko, ndico copatulikitsa pa malire a Alevi.
13 Ndipo polingana ndi malire a ansembe Alevi akhale nalo gawo la zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace; m'litali mwace monse ndimo zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwace zikwi khumi.
14 Ndipo asagulitseko, kapena kulisintha, kapena kupitiriza zipatso zoyamba za dziko; pakuti liri lopatulika la Yehova.
15 Ndipo zikwi zisanu zotsalazo m'kupingasa kwace, cakuno ca zikwi makumi awiri mphambu zisanu, zikhale za nchito wamba za mudzi, za kumangapo zapabusa; ndi mudzi ukhale pakati pace.
16 Ndi miyeso yace ndi iyi: mbali ya kumpoto, mabango zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumwela, zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kummawa, zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumadzulo, zikwi zinai mphambu mazana asanu.
17 Ndipo mudziwo ukhale ndi busa lace; kumpoto mabango mazana awiri mphambu makumi asanu, kumwela mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kum'mawa mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kumadzulo mazana awiri mphambu makumi asanu.
18 Ndipo madera otsalawo m'litali mwace alingane ndi copereka copatulika, ndico zikwi khumi kum'mawa, ndi zikwi khumi kumadzulo, alingane ndi copereka copatulika; ndi zipatso zace zikhale za cakudya ca iwo ogwira nchito m'mudzi.
19 Iwo ogwira nchito m'mudzi mwa mafuko onse a Israyeli alimeko.
20 Copereka conse ndico mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwace; mucipereke copereka copatulika camphwamphwa, pamodzi ndi dziko la mudziwo.
21 Ndipo madera ena otsalawo ndiwo a kalonga, mbali yina ndi yina ya copereka copatulika ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa zikwi makumi awiri mphambu zisanu za copereka ku malire a kum'mawa, ndi kumadzulo kutsogolo kwa zikwi makumi awiri mphambu zisanu ku malire a kumadzulo, pandunji pa magawo enawo ndiwo ca kalonga; ndipo copereka copatulika ndi malo opatulika a kacisi zidzakhala pakati pace.
22 Kuyambira tsono dziko la Alevi kufikira dziko la mudzi, ndiwo a pakati pa magawo ace a kalonga, pakati pa malire a Yuda ndi malire a Benjamini, kukhale kwa kalonga.
23 Kunena za mafuko otsala tsono, kuyambira ku mbali ya kum'mawa kufikita mbali ya kumadzulo, Benjamini akhale nalo gawo limodzi.
24 Ndi ku malire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi.
25 Ndi ku malire a Simeoni kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Isakara, limodzi.
26 Ndi ku malire a Isakara, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Zebuloni, limodzi.
27 Ndi ku malire a Zebuloni, kuyambira ku mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Gadi, limodzi.
28 Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwela, kuloza kumwela, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati ndi Kadesi, ku mtsinje wa Aigupto, kufikira ku nyanja yaikuru.
29 Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israyeli ndi kucita maere, likhale colowa cao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova.
30 Ndipo malekezero a mudzi ndi awa: mbali ya kumpoto avese mabango zikwi zinai mphambu mazana asanu;
31 ndi zipata za mudzi zidzakhala monga mwa maina a mafuko a Israyeli; zipata zitatu kumpoto: cipata cimodzi ca Rubeni, cipata cimodzi ca Yuda, cipata cimodzi ca Levi;
32 ndi ku mbali ya kum'mawa zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: cipata cimodzi ca Yosefe, cipata cimodzi ca Benjamini, cipata cimodzi ca Dani;
33 ndi ku mbali ya kumwela ayese zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: cipata cimodzi ca Simeoni, cipata cimodzi ca Isakara, cipata cimodzi ca Zebuloni;
34 ku mbali ya kumadzulo zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zace zitaru; cipata cimodzi ca Gadi, cipata cimodzi ca Aseri, cipata cimodzi ca Nafitali.
35 Pozungulira pace ndipo mabango zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mudziwo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.