Ezekieli 37 BL92

Masomphenya a mafupa

1 Dzanja la Yehova linandikhalira, ndipo anaturuka nane mu mzimu wa Yehova, nandiika m'kati mwa cigwa, ndico codzala ndi mafupa;

2 ndipo anandipititsa pamenepo pozungulira ponse, ndipo taonani, anali aunyinji pacigwa pansi, ndipo anaumitsitsa.

3 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, mafupa awa nkukhala ndi moyo kodi? Ndipo ndinati, Ambuye Yehova, mudziwa ndinu.

4 Pamenepo anati kwa ine, Nenera kwa mafupa awa, nuti nao, Mafupa ouma inu, imvani mau a Yehova.

5 Atero Ambuye Yehova kwa mafupa awa, Taonani, ndidzalonga mpweya mwa inu, ndipo mudzakhala ndi moyo.

6 Ndipo ndidzakuikirani mtsempha, ndi kufikitsira inu mnofu, ndi kukuta inu ndi khungu, ndi kulonga mpweya mwa inu; ndipo mudzakhala ndi moyo; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehoya.

7 M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobede gobede, ndi mafupa anasendererana, pfupa kutsata pfupa linzace.

8 Ndipo ndinapenya, taonani, panali mitsempha pa iwo, panadzaponso mnofu, ndi khungu linawakuta pamwamba pace; koma munalibe mpweya mwa iwo.

9 Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kucokera ku mphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.

10 M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira ciriri, gulu la nkhondo lalikurukuru ndithu.

11 Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israyeli; taonani, akuti, Mafupa athu auma, ciyembekezo cathu catayika, talikhidwa.

12 Cifukwa cace, nenera, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani anthu anga, ndidzatsegula kumanda kwanu, ndi kukweza inu muturuke m'manda mwanu, ndipo ndidzakulowetsani m'dziko la Israyeli.

13 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine. Yehova potsegula Ine kumanda kwanu, ndi kukweza inu kukuturutsani m'manda mwanu, anthu anga inu.

14 Ndipo ndidzalonga mzimu wanga mwa inu, nimudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzakukhazikani m'dziko mwanu; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena ndi kucicita, ati Yehova.

15 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

16 Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israyeli anzace; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efraimu, ndi wa nyumba yonse ya Israyeli anzace;

17 nuiphatikize wina ndi unzace ikhale mtengo umodzi m'dzanja lako.

18 Ndipo ana a anthu amtundu wako akanena ndi iwe, ndi kuti, Sutifotokozera nanga zitani izi?

19 unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efraimu, ndi wa mafuko a Israyeli anzace, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa.

20 Ndipo mitengo imene ulembapo idzakhala m'dzanja mwako pamaso pao.

21 Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israyeli pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa ku mbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;

22 ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israyeli; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.

23 Ndipo sadzadzidetsanso ndi mafano ao, kapena ndi zonyansa zao, kapena ndi zolakwa zao ziri zonse; koma ndidzawapulumutsa mokhala mwao monse m'mene anacimwamo, ndi kuwayeretsa; m'mwemo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.

24 Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m'maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwacita.

25 Ndipo adzakhala m'dziko ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga, limene anakhalamo makolo anu, ndipo adzakhala m'mwemo iwo, ndi ana ao, ndi zidzukulu zao kosatha; ndi Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wao kosatha.

26 Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwacurukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.

27 Kacisi wanganso adzakhala nao, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

28 Ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakupatula Israyeli, pokhala pakati pao malo anga opatulika kosatha.