1 NDIPO kunali caka ca makumi atatu, mwezi wacinai, tsiku lacisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.
2 Tsiku lacisanu la mwezi, ndico caka cacisanu ca kutengedwa ndende mfumu Yoyakini,
3 anadzadi mau a Yehova kwa Ezekieli wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Akasidi kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.
4 Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wocokera kumpoto, mtambo waukuru ndi moto wopfukusika m'mwemo, ndi pozungulira pace padacita ceza, ndi m'kati mwace mudaoneka ngati citsulo cakupsa m'kati mwa moto.
5 Ndi m'kati mwace mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,
6 ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai.
7 Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi ku mapazi ao kunanga kuphazi kwa mwana wa ng'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.
8 Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao.
9 Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; ciri conse cinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.
10 Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya ku dzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya ciombankhanga.
11 Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; ciri conse cinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.
12 Ndipo zinayenda, ciri conse cinalunjika kutsogolo kwace uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuka poyenda.
13 Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makara amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unacita ceza, ndi m'motomo mudaturuka mphezi.
14 Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima.
15 Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodzi imodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai.
16 Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.
17 Poyenda zinayenda ku mbali zao zinai, zosatembenuka poyenda.
18 Ndi mikombero yace inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao.
19 Ndipo poyenda zamoyozo, njingazi zinayenda pambali pao; ndipo ponyamuka pansi zamoyozo, njinga zinanyamuka.
20 Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izo; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m'njingazo.
21 Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izi; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izo; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi.
22 Ndi pa mitu ya zamoyozi panali cifaniziro ca thambo, monga mawalidwe a krustalo woopsa, loyalika pamwamba pamitu pao.
23 Ndi pansi pa thambolo mapiko ao analunjikana, lina kulunjika ku linzace; ciri conse cinali nao mapiko awiri akuphimba matupi ao, cakuno ndi cauko.
24 Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi akulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao.
25 Ndipo panamveka mau pamwamba pa thambolo linali pamwamba pa mitu yao; pakuima izi zinagwetsa mapiko ao.
26 Ndi pamwamba pa thambo linali pamitu pao panali cifaniziro ca mpando wacifumu, maonekedwe ace ngati mwala wa safiro; ndipo pa cifaniziro ca mpando wacifumu panali cifaniziro ngati maonekedwe ace a munthu wokhala pamwamba pace.
27 Ndipo ndinapenya ngati citsulo cakupsa, ngati maonekedwe ace a moto m'kati mwace pozungulira pace, kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kumwamba kwace; ndipo kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kunsi kwace ndinaona ngati maonekedwe ace a moto; ndi kunyezimira kudamzinga.
28 Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwace pozungulira pace. Ndiwo maonekedwe a cifaniziro ca ulemerero wa Yehova. Ndipo pakucipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.