Ezekieli 45 BL92

Cigawo ca dziko

1 Ndipo pogawa dziko likhale calowa cao, mupereke copereka kwa Yehova, ndico gawo lopatulika la dziko; m'litali mwace likhale la mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwace zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ace onse pozungulira pace.

2 Kutengako malo opatulika akhale nayo mikono mazana asanu m'litali mwace, ndi mazana asanu kupingasa kwace, lamphwamphwa pozungulira pace; ndi pabwalo pace poyera pozungulira pace mikono makumi asanu.

3 Ndipo kuyambira poyesedwapo uyese zikwi makumi awiri mphambu zili sanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace; m'menemo ndimo mukhale malo opatulika, ndiwo opatulika, ndiwo opatulikitsa.

4 Ndilo gawo lopatulika la dziko, ndilo la ansembe atumiki a malo opatulika, amene ayandikira kutumikira Yehova; apo ndipo amange nyumba zao, likhale malo a pa okha a: kwa malo opatulika.

5 Ndipo zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace, ndilo gawo la Alevi, atumiki a kacisi; likhale lao lao la midzi yokhalamo.

6 Ndipo dziko lace la mudziwo mulipereke la zikwi zisanu kupingasa kwace, ndi zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, pa mbali ya cipereko copatulika, ndilo la nyumba yonse ya Israyeli.

7 Ndipo kalonga adzakhala nalo gawo lace mbali yina ndi mbali inzace ya cipereko copatulika, ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa cipereko copatulika, ndi kutsogolo kwa dziko la mudzi, mbali ya kumadzulo kumadzulo, ndi mbali ya kum'mawa kum'mawa; ndi m'litali mwace mudzalingana ndi limodzi la magawo, kuyambira ku malire a kumadzulo kufikira malire a kum'mawa.

8 M'dzikomo ili lidzakhala lace lace m'Israyeli; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israyeli monga mwa mapfuko ao.

9 Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israyeli inu, lekani kucita ciwawa, ndi kulanda za eni ace; mucite ciweruzo ndi cilungamo; lekani kupitikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova.

10 Muzikhala nayo miyeso yoona, ndi efa woona, ndi bati loona.

11 Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri.

12 Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo mane wanu.

13 Copereka mucipereke ndico limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa tirigu; muperekenso limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa barele;

14 ndi gawo lonenedwa la mafuta, la bati wa mafuta, ndilo limodzi la magawo khumi la bati, kulitapa pa kori; ndiwo mabati khumi, ndiwo homeri; pakuti mabati khumi ndiwo homeri;

15 ndi mwana wa nkhosa mmodzi wa zoweta, kumtenga pa mazana awiri wocokera ku madimba a Israyeli, ndiye wa nsembe yaufa, ndi wa nsembe yopsereza, ndi wa nsembe zoyamika, kuwacitira cotetezera, ati Ambuye Yehova.

16 Anthu onse a m'dziko azipereka copereka ici cikhale ca kalonga wa m'Israyeli.

17 Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pamadyerero, ndi pokhala mwezi, ndi pamasabata; pa madyerero onse oikika a nyumba ya Israyeli; ndipo apereke nsembe yaucimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kucitira cotetezera nyumba ya Israyeli.

Nsembe ya pa mwezi woyamba

18 Atero Ambuye Yehova, Mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, uzitenga mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndipo uyeretse malo opatulika.

19 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo, naupake pa mphuthu za kacisi, ndi pa ngondya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za cipata ca bwalo lam'kati.

20 Tsiku lacisanu ndi ciwiri la mweziwo ucitire momwemo ali yense wolakwa ndi wopusa; motero mucitire kacisiyo comtetezera.

Za Paskha

21 Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi, muzicita Paskha, madyerero a masiku asanu ndi awiri; audye mkate wopanda cotupitsa.

22 Ndipo tsiku lomwelo kalonga adzikonzere yekha ndi anthu onse a m'dziko ng'ombe, ikhale ya nsembe yaucimo.

23 Ndipo masiku asanu ndi awiri a madyerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda cirema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yaucimo.

24 Nakonze nsembe yaufa, ku ng'ombe kukhale efa; ndi ku nkhosa yamphongo kukhale efa; ndi kuefa kukhale hini wa mafuta.

25 Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi, pamadyerero, acite momwemo masiku asanu ndi awiri, monga mwa nsembe yaucimo, monga mwa nsembe yopsereza, ndi monga mwa nsembe yaufa, ndi monga mwa mafuta.