1 Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko.
3 Potero wobadwa ndi munthu iwe, udzikonzeretu akatundu a pa ulendo wa kundende, nucoke usana pamaso pao, ucoke pakhala iwepo kumka malo ena pamaso pao; kapena adzacizindikira, angakhalendiwo nyumbayopanduka.
4 Uziturutsa akatundu ako usana pamaso pao, ngati a pa ulendo wa kundende; ndipo madzulo uzituruka wekha pamaso pao, monga amaturuka olowa kundende.
5 Udziboolere khoma pamaso pao, nuwaturutsire akatundu pamenepo,
6 Pamaso pao uwasenze paphewa pako, ndi kuwaturutsa kuli mdima, nuphimbe nkhope yako kuti usapenye dziko; popeza ndakuika cizindikilo ca nyumba ya Israyeli.
7 Ndipo ndinacita monga momwe anandilamulira, ndinaturutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawaturutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso: pao.
8 Ndipo m'mawa mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,
9 Wobadwa ndi munthu iwe, kodi nyumba ya Israyeli, nyumba yampanduko, siinati kwa iwe. Ucitanji?
10 Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Katundu uyu anena za kalonga wa m'Yerusalemu, ndi nyumba yonse ya Israyeli yokhala pakati pao.
11 Uziti, Ine ndine cizindikilo canu, monga ndacita ine momwemo kudzacitidwa nao; adzacotsedwa kumka kundende.
12 Kalongayo ali pakati pao adzasenza paphewa pace mumdima, nadzaturuka; adzaboola palinga, nadzaturutsapo; adzaphimba nkhope yace kuti asapenye dziko ndi maso ace.
13 Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babulo, ku dziko la Akasidi; sadzaliona, cinkana adzafako.
14 Ndipo onse omzinga kumthandiza, ndi magulu ace onse, ndidzawamwaza ku mphepo zonse, ndidzawasololeranso lupanga lakuwatsata.
15 Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwamwaza Ine mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.
16 Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
17 Anandidzeranso mau a Mulungu, akuti,
18 Wobadwa ndi munthu iwe, udye mkate wako ndi kunthunthumira, ndi kumwa madzi ako ndi kunjenjemera, ndi kutenga nkhawa;
19 nunene kwa anthu a m'dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala m'Yerusalemu, ndi za dziko la Israyeli, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lacipululu, kuleka kudzala kwace cifukwa ca ciwawa ca onse okhalamo.
20 Ndi midzi yokhalamo anthu idzapasuka, ndi dziko lidzakhala labwinja; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
21 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
22 Wobadwa ndi munthu iwe, ngwotani mwambi umene muli nao m'dziko la Israyeli, wakuti, Masiku acuruka, ndi masomphenya ali onse apita pacabe?
23 Cifukwa cace unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzauchulanso mwambi m'Israyeli; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzacitika masomphenya ali onse.
24 Pakuti sikudzakhalanso masomphenya acabe, kapena ula wosyasyalika m'nyumba ya Israyeli.
25 Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzacitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwacita, ati Yehova Mulungu.
26 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
27 Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israyeli akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri: ndipo anenera za nthawi ziri kutali,
28 Cifukwa cace uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzacitika, ati Ambuye Yehova.