1 Ndipo mau a Yehova anandidzera, kuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku mapiri a Israyeli, uwanenere,
3 nunene, Mapiri a Israyeli inu, tamverani mau a Yehova Mulungu: Atero Yehova Mulungu kwa mapiri ndi zitunda, kwa mitsinje ndi zigwa, Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzaononga misanje yanu.
4 Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.
5 Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israyeli pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.
6 Pokhala inu ponse midzi idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi nchito zanu zifafanizidwe.
7 Ndi ophedwa adzagwa pakati panu, matero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
8 Koma ndidzasiyapo otsala, popeza mudzakhala nao ena akupulumuka lupanga mwa amitundu pobalalitsidwa inu m'maiko maiko.
9 Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukila Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wacigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao acigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, cifukwa ca zoipa anazicita m'zonyansa zao zonse.
10 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, sindinanena cabe kuti ndidzawacitira coipa ici.
11 Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, cifukwa ca zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israyeli; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri.
12 Wokhala kutali adzafa ndi mliri, wakhala pafupi adzagwa ndi lupanga; koma wotsala ndi kuzingidwa adzafa ndi njala; momwemo ndidzawakwaniritsira ukali wanga,
13 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu ali yense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse.
14 Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa cipululu ca ku Dibla mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.