1 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzitengere mpeni wakuthwa, ndiwo lumo la wometa, udzitengere ndi kulipititsa pamutu pako ndi pa ndebvu zako; nudzitengere muyeso kuyesa nao, ndi kugawa tsitsilo.
2 Limodzi la magawo ace atatu utenthe ndi moto pakati pa mudzi pakutha masiku a kuzingidwa mudzi, nutenge gawo lina ndi kukwapula-kwapula ndi lupanga pozungulira pace, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.
3 Utengekonso owerengeka ndi kuwamanga m'mkawo wa maraya ako.
4 Nutengekonso pa amenewa ndi kuwaponya pakati pa moto, ndi kuwatentha m'moto; kucokera kumeneko udzaturuka moto pa nyumba yonse ya Israyeli.
5 Atero Yehova Mulungu, Uwu ndi Yerusalemu ndinauika pakati pa amitundu, ndi pozungulira pace pali maiko.
6 Koma anakaniza maweruzo anga ndi kucita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendamo.
7 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayenda m'malemba anga, kapena kucita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawacita;
8 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatsutsana nawe Inedi, ndi kucita maweruzo pakati pako pamaso pa amitundu.
9 Ndipo ndidzacita mwa iwe cimene sindinacicita ndi kale lonse, ndi kusadzacitanso momwemo, cifukwa ca zonyansa zako zonse.
10 Cifukwa cace atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzacita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse.
11 M'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, popeza wadetsa malo anga opatulika ndi zonyansa zako zonse ndi zoipsa zako zonse, ndidzakucepsa; diso langa silidzalekerera, ndi Inenso sindidzacita cifundo.
12 Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa ku mphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.
13 Motero mkwiyo wanga udzakwaniridwa, ndipo ndidzakhutitsa ukali wanga pa iwo, ndi kudzitonthoza; ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova ndinanena m'cangu canga, pokwaniridwa nao ukali wanga.
14 Ndidzakuikanso ukhale bwinja ndi cotonza pakati pa amitundu akukuzinga, pamaso pa onse akupitirirapo.
15 Momwemo cidzakhala cotonza ndi mnyozo, cilangizo ndi codabwiza kwa amitundu akukuzinga, pamene ndikucitira maweruzo mu mkwiyo ndi ukali ndi madzudzulo aukali; Ine Yehovandanena.
16 Pakuwatumizira Ine mibvi yoipa ya njala yakuononga, imene ndidzatumiza kukuonongani, pamenepo ndidzakukuzirani njala, ndi kukutyolerani mcirikizo, ndiwo cakudya.
17 Inde ndidzakutumizirani njala ndi zirombo, ndipo zidzakusowetsa ana ako; ndi mliri ndi mwazi zidzakugwera; ndidzakufikitsiranso lupanga; Ine Yehova ndacinena.