Ezekieli 10 BL92

Masomphenya a akerubi

1 Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, ku thambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a cifaniziro ca mpando wacifumu pamwamba pao.

2 Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wobvala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makara a moto ocokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mudzi. Nalowa, ndiri cipenyere ine.

3 Tsono akerubi anaima ku dzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzara bwalo la m'kati.

4 Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kucokera kukerubi kumka ku ciundo ca nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi ceza ca ulemerero wa Yehova.

5 Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye.

6 Ndipo kunali pomlamulira munthu wobvala bafutayo, ndi kuti, Para moto pakati pa njingazi ndi pakati pa akerubi; iye analowa, naima m'mbali mwa njinga.

7 Pamenepo kerubi wina anatambasula dzanja lace pakati pa akerubi ku moto uli pakati pa akerubi, naparako, nauika m'manja mwa iye wobvala bafuta, ndiye naulandita, naturuka.

8 Ndipo panaoneka pa akerubi conga dzanja la munthu pansi pa mapiko ao.

9 Pamenepo ndinapenya, ndipo taonani, njinga zinai m'mbali mwa akerubi, njinga imodzi m'mbali mwa kerubi mmodzi, ndi njinga yina m'mbali mwa kerubi wina, ndi maonekedwe a njingazi ananga mawalidwe a berulo.

10 Ndipo maonekedwe ace, zonse zinai zinafanana, ngati njinga ziwiri zopingasitsana,

11 Pakuyenda akerubi anayenda ku mbali zao zinai, sanatembenuka poyenda; koma komwe udalozako mutu anatsatako, sanatembenuka poyenda.

12 Ndipo thupi lao lonse, ndi misana yao, ndi manja ao, ndi mapiko ao, ndi njinga zomwe, zinadzala ndi maso pozungulira pao, zingakhale njingazi anai aja anali nazo.

13 Kunena za njingazi, wina anazipfuulira, ndiri cimvere ine, Kunkhulirani.

14 Ndipo ali yense anali nazo nkhope zinai, nkhope yoyamba ndiyo nkhope ya kerubi, ndi nkhope yaciwiri ndiyo nkhope ya munthu, ndi yacitatu ndiyo nkhope ya mkango, ndi yacinai ndiyo nkhope ya ciombankhanga.

15 Pamenepo akerubi anakwera, ndizo zamoyo zija ndinaziona kumtsinje Kebara.

16 Ndipo pakuyenda akerubi, njinga zinayenda pambali pao, ndi pakutambasula mapiko ao akerubiwo kuuluka padziko, njingazi sizinatembenuka pambali pao.

17 Pakuima iwo zinaima izi, ndi pakukwera iwo izi zinakwera pamodzi nao; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mwa izo.

18 Ndipo ulemerero wa Yehova unacoka pa ciundo ca nyumba, nuima pamwamba pa akeruibi.

19 Ndipo akerubi anatambasula mapiko ao, nauluka padziko, ndiri cipenyere, pakucoka iwo ndi njingazi pa mbali pao; ndipo anaima pa citseko ca cipata ca kum'mawa ca nyumba ya Yehova, ndi ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unali pamwamba pao.

20 Awa ndi zamoyozo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israyeli kumtsinje Kebara, ndipo ndinadziwa kuti ndiwo akerubi.

21 Yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense mapiko anai, ndi cifaniziro ca manja a munthu pansi pa mapiko ao.

22 Ndi cifaniziro ca nkhope zao ndico nkhope zomwezo ndinaziona kumtsinje Kebara, maonekedwe ao ndi iwo eni; ali yense anayenda, nalunjika m'tsogolo.