Ezekieli 18 BL92

Udindo ndi wace wace wa munthu

1 Ndipo anandidzera mau a Yehoya, akuti,

2 Mutani inu ndi kunena mwambi uwu za dziko la Israyeli, wakuti, Atate adadya mphesa zosacha, ndi mano a ana ayayamira.

3 Pali Ine, ati Ambuye Yehova, simudzaonanso cifukwa ca kunena mwambiwu m'Israyeli.

4 Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wocimwawo ndiwo udzafa.

5 Koma munthu akakhala wolungama, nakacita ciweruzo ndi cilungamo,

6 wosadya pamapiripo, wosakweza maso ace ku mafano a nyumba ya Israyeli, wosaipsa mkazi wa mnansi wace, kapena kuyandikira mkazi ataoloka,

7 wosasautsa munthu ali yense, koma wambwezera wangongole cigwiriro cace, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala cakudya cace, nabveka wamarisece ndi cobvala,

8 wosapereka molira phindu, wosatenga coonjezerapo wobweza dzanja lace lisacite cosalungama, woweruza zoona pakati pa munthu ndi mnzace,

9 amayenda m'malemba anga, nasunga maweruzo anga kucita cokhulupirika; iye ndiye wolungama, adzakhala ndi moyo ndithu, anena Ambuye Yehova.

10 Akabala mwana ndiye mkhungu, wokhetsa mwazi, wocita cimodzi ca izi,

11 wosacita zabwino zonse zija, koma anadyanso pamapiri, naipsa mkazi wa mnansi wace,

12 nasautsa osauka ndi osowa, natenga zofunkha, wosabwezera cigwiriro, nakweza maso ace kumafano, nacita conyansa,

13 napereka molira phindu, nalandira coonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? sadzakhala ndi moyo, anacita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, niwazi wace umkhalira.

14 Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zocimwa zonse adazicita atate wace, naopa wosacita zoterezo,

15 wosadya pamapiri, kapena kukweza maso ace ku mafano a nyumba ya Israyeli, wosaipsa mkazi wa mnansi wace,

16 kapena kusautsa wina ali yense, wosatenga cigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala cakudya cace, nabveka wamarisece ndi cobvala,

17 naletsa dzanja lace pa wozunzika, wosalandira phindu kapena coonjezerapo, wocita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wace, adzakhala ndi moyo ndithu.

18 Atate wace, popeza anazunza cizunzire, nafunkha za mbale wace, nacita cimene siciri cabwino pakati pa anthu ace, taona, adzafa mu mphulupulu yace.

19 Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wace? Mwanayo akacita ciweruzo ndi cilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwacita, adzakhala ndi moyo ndithu.

20 Moyo wocimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu zaatate wace, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; cilungamo ca wolungama cidzamkhalira, ndi coipa ca woipa cidzamkhalira,

21 Koma woipayo akabwerera kusiya macimo ace onse adawacita nakasunga malemba anga onse, ndi kucita ciweruzo ndi cilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

22 Nnena cimodzi conse ca zolakwa zace zonse adazicita cidzakumbukika cimtsutse; m'cilungamo cace adacicita adakhala ndi moyo.

23 Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yace, ndi kukhala ndi moyo?

24 Koma wolungamayo akabwerera kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, ndi kucita monga mwa zonyansa zonse azicita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena cimodzi ca zolungama zace zonse adzazicita cidzakumbukika m'kulakwa kwace analakwa nako, ndi m'kucimwa kwace anacimwa nako; momwemo adzafa.

25 Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israyeli, Kodi njira yanga njosayenera? njira zanu si ndizo zosayenera?

26 Wolungamayo akatembenukira kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, adzafa momwemo; m'mphulupulu yace adaicita adzafa.

27 Ndipo woipayo akatembenukira kuleka coipa cace adacicita, nakacita ciweruzo ndi cilungamo, adzapulumutsa moyo wace.

28 Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zace zonse adazicita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

29 Koma nyumba ya Israyeli imanena, Njira ya Ambuye njosayenera, Inu, nyumba ya Israyeli, kodi njira zanga nzosayenera? njira zanu si ndizo zosayenera?

30 Cifukwa cace ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israyeli, yense monga mwa njira zace, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.

31 Tayani, ndi kudzicotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israyeli?

32 Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; cifukwa cace bwererani, nimukhale ndi moyo.