1 Caka cakhumi, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi ndi ciwiri la mweziwo, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa: nkhope yako itsutsane naye Farao mfumu ya Aigupto, nunenere motsutsana ndi iye, ndi Aigupto lonse;
3 nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aigupto, ng'ona yaikuru yakugona m'kati mwa mitsinje yace, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu.
4 Koma ndidzaika mbedza m'kamwa mwako, ndi kumamatiritsa nsomba za m'mitsinje mwako ku mamba ako; ndipo ndidzakukweza kukuturutsa m'kati mwa mitsinje yako, pamodzi ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako zomamatira pa mamba ako.
5 Ndipo ndidzakutaya kucipululu, iwe ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako; udzagwa kuthengo koyera, sudzaunjikidwa, kapena kuoledwa; ndakupereka ukhale cakudya ca zirombo za padziko, ndi mbalame za kumlengalenga,
6 Ndi onse okhala m'Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anakhalira nyumba ya Israyeli mcirikizo wabango.
7 Muja anakugwira ndi dzanja unatyoka, ndi kulasa mapewa ao onse; ndi muja anakutsamira unatyoka, ndi kuwagwedeza ziuno zao zonse.
8 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, ndikudzera ndi lupanga, ndi kukulikhira munthu ndi nyama.
9 Ndi dziko la Aigupto lidzakhala lopasuka ndi labwinja; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anati, Mtsinjewo ndi wanga, ndinaulenga ndine.
10 Cifukwa cace taona, nditsutsana ndi iwe ndi mitsinje yako, ndipo ndidzasandutsa dziko la Aigupto likhale lopasuka konse, ndi labwinja, kuyambira nsanja ya Sevene kufikira malire a Kusi.
11 Silidzapitamo phazi la munthu, kapena phazi la nyama losapitamo, losakhalamo anthu zaka makumi anai.
12 Ndipo ndidzasandutsa dziko la Aigupto labwinja pakati pa maiko a mabwinja; ndi midzi yace pakati pa midzi yopasuka idzakhala yabwinja zaka makumi anai; ndipo ndidzamwaza Aaigupto mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.
13 Pakuti atero Ambuye Yehova, Zitatha zaka makumi anai ndidzasonkhanitsa Aaigupto ku mitundu ya anthu kumene anamwazikirako;
14 ndipo ndidzabweza undende wa Aigupto, ndi kuwabwezera ku dziko la Patro, ku dziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka,
15 Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawacepsa, kuti asacitenso ufumu pa amitundu.
16 Ndipo sudzakhalanso cotama ca nyumba ya Israyeli, kukumbutsa mphulupulu, pakuwatembenukira kuwatsata; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
17 Ndipo kunali caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
18 Wobadwa ndi munthu iwe, Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anacititsa ankhondo ace nchito yaikuru yoponyana ndi Turo; mitu yonse inacita dazi, ndi mapewa onse ananyuka; koma analibe kulandira mphotho ya ku Turo, iye kapena ankhondo ace, pa nchito anagwirayo;
19 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzapereka dziko la Aigupto kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzacoka nao aunyinji ace, nadzafunkha ndi kulanda zace, ndizo mphotho ya khamu lace.
20 Ndamninkha dziko la Aigupto combwezera nchito yace, popeza anandigwirira nchito, ati Ambuye Yehova.
21 Tsiku ilo ndidzameretsera nyumba ya Israyeli nyanga; ndipo ndidzakutsegulira pakamwa pakati pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.