Ezekieli 25 BL92

Aneneratu za kulangidwa kwa Aamoni

1 Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kwa ana a Amoni, nuwanenere;

3 nunene kwa ana a Amoni, Tamverani mau a Ambuye Yehova, Atero Ambuye Yehova, Popeza unati, Onyo, kunena malo anga opatulika; muja anadetsedwa ndi kunena dziko la Israyeli; muja linapasuka ndi kunena nyumba ya Yuda; muja adalowa kundende;

4 cifukwa cace taona, ndidzakupereka kwa ana a kum'mawa ukhale wao wao, kuti amange misasa yao mwa iwe, namange pokhala pao mwa iwe, iwo adzadya zipatso zako ndi kumwa mkaka wako.

5 Ndipo ndidzayesa Raba khola la ngamira, ndi ana a Amoni popumula zoweta zazing'ono; matero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

6 Pakuti atero Ambuye Yehova, Waomba manja, ndi kubvina, ndi kukondwera ndi cipeputso conse ca moyo wako, kupeputsa dziko la Israyeli,

7 cikufwa cace taona, ndakutambasulira dzanja langa, ndipo ndidzakupereka ukhale cofunkha ca amitundu, ndi kukudula mwa mitundu ya anthu, ndi kukutayikitsa m'maiko, ndidzakuononga; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Za kulangidwa kwa Moabu

8 Atero Ambuye Yehova, Popeza Moabu ndi Seiri akuti, Taona nyumba ya Yuda ikunga amitundu onse;

9 cifukwa cace taona, ndidzatsegula pambali pace pa Moabu kuyambira ku midzi, ku midzi yace yokhala mphepete, yokometsetsa ya m'dziko, Betiyesimoti, Baalameoni, ndi Kiriataimu,

10 kuwapereka kwa ana a kum'mawa pamodzi ndi ana a Amoni; ndipo ndidzawapereka akhale ao ao, kuti ana a Amoni asakumbukikenso mwa amitundu;

11 ndipo ndidzakwaniritsa maweruzo m'Moabu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Za kulangidwa kwa Edomu

12 Atero Ambuye Yehova, Popeza Edomu anacita mobwezera cilango pa nyumba ya Yuda, naparamula kwakukuru pakuibwezera cilango,

13 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndidzatambasulira Edomu dzanja langa, ndi kulilikhira munthu ndi nyama, ndi kulisandutsa labwinja; kuyambira ku Temani mpaka Dedani adzagwa ndi lupanga.

14 Ndipo ndidzalibwezera Edomu cilango mwa dzanja la anthu anga Israyeli; ndipo adzacita m'Edomu monga mwa mkwiyo wanga, ndi ukali wanga; motero adzadziwa kubwezera cilango kwanga, ati Ambuye Yehova.

Za kulangidwa kwa Afilisti

15 Atero Ambuye Yehova, Popeza Afilisti anacita mobwezera cilango nabwezera cilango ndi mtima wopeputsa kuononga, ndi udani wosatha,

16 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatambasulira Afilisti dzanja langa, ndi kulikha. Akereti, ndi kuononga otsalira mphepete mwa nyanja.

17 Ndipo ndidzawabwezera cilango cacikuru, ndi malango ankharwe; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwabwezera cilango Ine.