Ezekieli 32 BL92

Nyimbo ya maliro ya pa Farao

1 Ndipo kunali caka cakhumi ndi ciwiri, mwezi wakhumi ndi ciwiri, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, takwezera Farao mfumu ya Aigupto nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango wa amitundu, unanga ng'ona ya m'nyanja, unabuka m'mitsinje mwako, nubvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao.

3 Atero Ambuye Yehova, Ndidzakuponyera khoka langa mwa msonkhano wa mitundu yambiri ya anthu, nadzakubvuulira m'khoka mwanga.

4 Ndipo ndidzakusiya pamtunda, ndidzakuponya kuthengo koyera, ndi kuteretsa pa iwe mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi kukhutitsa zirombe za dziko lonse lapansi ndi iwe.

5 Ndipo ndidzaika nyama yako pamapiri, ndi kudzaza zigwa ndi msinkhu wako.

6 Ndipo ndidzamwetsa dziko losambiramo iwe ndi mwazi wako, kufikira kumapiri; ndi mitsinje idzadzala nawe.

7 Ndipo pakukuzima iwe ndidzaphimba thambo, ndi kudetsa nye nyezi zace; ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwace.

8 Ndidzakudetsera miyuni ronse yakuunikira kuthambo, ndi kucititsa mdima pa dziko lako, ati Ambuye Yehova.

9 Ndidzabvutanso mitima ya mitundu yambiri ya anthu, pakufikitsa Ine cionongeko cako mwa amitundu, m'maiko amene sunawadziwa.

10 Ndipo ndidzasumwitsa nawe mitundu yambiri ya anthu, ndi mafumu ao adzacita malunga cifukwa ca iwe, pakung'animitsa Ine lupanga langa pamaso pao; ndipo adzanjenjemera mphindi zonse, yense cifukwa ca moyo wace tsiku lakugwa Iwe,

11 Pakuti atero Ambuye Yehova, Lupanga la mfumu ya ku Babulo lidzakudzera.

12 Ndidzagwetsa aunyinji ako ndi malupanga a eni mphamvu, ndiwo onse oopsetsa a amitundu; ndipo adzaipsa kudzikuza kwa Aigupto, ndi aunyinji ace onse adzaonongeka.

13 Ndidzaononganso nyama zace zonse za ku madzi ambiri; ndi phazi la munthu silidzabvundulira, ndi ziboda za nyama zosawabvundulira.

14 Pamenepo ndidzadikhitsa madzi ace, ndi kuyendetsa madzi a m'mitsinje mwao ngati mafuta, ati Ambuye Yehova.

15 Pakusanduliza Ine dziko la Aigupto likhale lopasuka ndi labwinja, dziko losowa zodzaza zace, pakukantha Ine onse okhala m'mwemo, pamenepo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.

16 Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana akazi a amitundu adzacita nayo maliro; adzalirira nayo Aigupto ndi aunyinji ace onse, ati Ambuye Yehova.

Mau a kulirira aunyinji a Aigupto

17 Kunalinso caka cakhumi ndi ciwiri, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi, anandidzera mau a Yehova, ndi kuti,

18 Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Aigupto, nuwagwetsere iye ndi ana akazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.

19 Uposa yani m'kukoma kwako? tsika, nuikidwe ndi osadulidwa.

20 Adzagwa pakati pa iwo ophedwa ndi lupanga, operekedwa kwa lupanga, mkokereko ndi aunyinji ace onse.

21 Amphamvu oposa ali m'kati mwa manda adzanena naye, pamodzi ndi othandiza ace, Anatsikira, agonako osadulidwawo, ophedwa ndi lupanga,

22 Asuri ali komwe ndi msonkhano wace wonse, manda ace amzinga; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga;

23 manda ao aikidwa ku malekezero a dzenje, ndi gulu lace lizinga manda ace; ophedwa onsewo adagwa ndi lupanga, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo.

24 Elamu ali komwe ndi gulu lace lonse lozinga manda ace; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwace kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.

25 Pakati pa ophedwa anamuikira kama, iye ndi aunyinji ace onse, manda ace amzinga, onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga, pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje, aikidwa pakati pa ophedwa,

26 Meseke, Tubala, ndi aunyinji ace onse ali komweko, manda ace amzinga; onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga; pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo.

27 Koma sagona pamodzi ndi amphamvu osadulidwa adagwawo amene anatsikira kumanda ndi zida zao za nkhondo, amene anawatsamiritsa malupanga ao; ndi mphulupulu zao ziri pa mafupa ao; pakuti anaopsetsa amphamvu m'dziko la amoyo.

28 Ndipo udzatyoledwa pakati pa osadulidwa, nudzagona pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga.

29 Edomu ali komwe, mafumu ace ndi akalonga ace onse, amene anaikidwa mu mphamvu yao, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga; agona pamodzi ndi osadulidwa, ndi iwo akutsikira kudzenje.

30 Akalonga a kumpoto ali komwe onsewo, ndi Azidoni onse, amene anatsikira pamodzi ndi ophedwa, nacita manyazi cifukwa ca kuopsetsa anacititsaku ndi mphamvu yao, nagona osadulidwa pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, nasenza manyazi ao pamodzi ndi iwo otsikira kudzenje.

31 Farao adzawaona, nadzasangalala nao aunyinji ace onse, Farao ndi ankhondo ace onse ophedwa ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.

32 Pakuti ndinaika kuopsa kwace m'dziko la amoyo; ndipo adzaikidwa pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, ndiye Farao ndi aunyinji ace onse, ali Ambuye Yehova.