1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Turo nyimbo ya maliro;
3 nuti kwa Turo, Iwe wakukhala polowera m'nyanja, wakucita malonda ndi mitundu ya anthu m'zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Turo, wati, Ine ndine wokongola wangwiro.
4 M'mphepete mwako muli m'kati mwa nyanja, iwo anakumanga iwe anakonza kukongola kwako kukhale kwangwiro.
5 Anaceka matabwa ako onse amlombwa wa ku Seniri, anatenga mikungudza ya ku Lebano kukupangira milongoti.
6 Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basana, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wocokera ku zisumbu za Kitimu.
7 Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Aigupto, likhale ngati mbendera yako; cophimba cako ndico nsaru yamadzi ndi yofiirira zocokera ku zisumbu za Elisa.
8 Okhala m'Zidoni ndi Arivadi ndiwo opalasa ako; anzeru ako, Turo, okhala mwa iwe, ndiwo oongolera ako.
9 Akr-ru a ku Gebala ndi eni luso ace anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amarinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.
10 Aperisiya, Aludi, Apuri, anali m'khamu lako; anthu ako a nkhondo anapacika cikopa ndi cisoti mwa iwe, anamveketsa kukoma kwako.
11 Anthu a Ativadi pamodzi ndi ankhondo ako anali pa malinga ako pozungulira, ndi Agamadi anali mu nsanja zako; anapacika zikopa zao pa makoma ako pozungulira, anakwaniritsa kukoma kwako.
12 Tarisi anagulana nawe malonda m'kucuruka kwa cuma ciri conse; anagula malonda ako ndi siliva ndi citsulo, seta ndi ntobvu.
13 Yavani, Tuba, Meseke, anagulana nawe malonda; ndi anthu amoyo ndi zotengera zamkuwa anagulana nawe malonda.
14 Iwo a nyumba ya Togarima anagula malonda ako ndi akavalo, ndi akavalo a nkhondo, ndi nyuru.
15 Anthu a ku Dedani anakutsatsa malonda, zisumbu zambiri zinazolowerana nawe malonda ako, anabwera nazo minyanga ndi phingo kugulana nawe malonda.
16 Aramu anacita nawe malonda cifukwa ca zambirizo udazipanga, anagula malonda ako ndi smaragido, nsaru yofiirira, ndi yopikapika, ndi bafuta, ndi korale, ndi ngale.
17 Yuda ndi dziko la Israyeli anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uci, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala.
18 Damasiko anagulana nawe malonda cifukwa ca zambirizo udazipanga, cifukwa ca kucuruka kwa cuma ciri conse, ndi vinyo wa ku Keliboni, ndi ubweya wa nkhosa woyera.
19 Vedani ndi Yavani anagula malonda ako ndi thonje, unagulana nao citsulo cosalala, ngaho, ndi mzimbe.
20 Dedani anagulana nawe malonda ndi nsaru za mtengo wace zoyenda nazo pa kavalo.
21 Arabu ndi akalonga onse a ku Kedara anazolowerana nao malonda ako; ana a nkhosa, nkhosa zamphongo, ndi mbuzi, izi anagulana nawe.
22 Amalonda a ku Seba ndi a ku Rama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa ziri zonse, ndi miyala iri yonse ya mtengo wace, ndi golidi.
23 Harani ndi Kane ndi Edene, amalonda a ku Seba Asuri ndi Kilimadi, anagulana nawe malonda.
24 Awa anagulana nawe malonda ndi zobvala zosankhika, ndi mitumba ya nsaru zofiirira ndi zopikapika, ndi cuma ca thonje lopotapota, ndi zingwe zopota zolimba za malonda ako.
25 Zombo za ku Tarisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzazidwa ndi cuma ndi ulemu waukuru pakati pa nyanja,
26 Opalasa ako anakufikitsa ku madzi akuru; mphepo ya kum'mawa inakutyola m'kati mwa nyanja,
27 Cuma cako, zako zogulana nazo malonda ako, amarinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m'kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako.
28 Pakumveka mpfuu wa oongolera ako mabwalo ako adzagwedezeka.
29 Ndi onse ogwira nkhafi, amarinyero, ndi oongolera onse a kunyanja, adzatsika ku zombo zao, nadzaima pamtunda,
30 nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira pfumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa,
31 nadzameta mpala, cifukwa ca iwe, nadzadzimangira ziguduli m'cuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.
32 Ndipo pakulira adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kukulirira, ndi kuti, Wakunga Turo ndani, wakunga uyu waonongeka pakati pa nyanja?
33 Pakuturuka malonda ako m'nyanja unadzaza mitundu yambiri ya anthu, unalemeretsa mafumu a pa dziko lapansi ndi cuma cako cocuruka ndi malonda ako.
34 Muja unatyoka ndi nyanja m'madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako.
35 Onse okhala pa zisumbu adagwa nawe, ndi mafumu ao aopsedwa kwambiri zikhululuka nkhope zao.
36 Amalonda mwa mitundu ya anthu akunyodola, wakhala coopsetsa iwe, ndipo sudzakhalanso konse.