Ezekieli 36 BL92

Aneneratu za mapiri a Israyeli

1 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, unenere kwa mapiri a Israyeli, uziti, Mapiri a Israyeli inu, imvani mau a Yehova.

2 Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Onyo, ingakhale misanje yakale iri yathu, colowa cathu;

3 cifukwa cace unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Cifukwa, inde cifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale colowa ca amitundu otsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;

4 cifukwa cace, mapiri inu a Israyeli, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi midzi yamabwinja, imene yakhala cakudya ndi coseketsa amitundu otsala akuzungulira;

5 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu lonse, amene anadzipatsira dziko langa likhale colowa cao ndi cimwemwe ca mtima wonse, ndi, mtima wopeputsa, kuti alande zace zonse zikhale zofunkha.

6 Cifukwa cace unenere za dziko la Israyeli, nuti kwa mapiri ndi kwa zitunda, kwa mitsinje ndi kwa zigwa, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndalankhula mu nsanje yanga ndi ukali wanga, popeza mwasenza manyazi a amitundu;

7 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndakweza dzanja langa Ine, ndi kuti, Zedi amitundu akuzungulira inu adzasenza manyazi ao.

8 Koma inu, mapiri a Israyeli, mudzaphukitsa nthambi zanu, ndi kubalira anthu anga Israyeli zipatso zanu, pakuti ayandikira kufika.

9 Pakuti taonani, Ine ndikhalira nanu kumodzi, ndipo ndidzakutembenukirani; ndipo mudzabzalidwa ndi kupaliridwa,

10 ndipo ndidzakucurukitsirani anthu nyumba yonse ya Israyeli, yonseyi, ndi m'midzimo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa midzi.

11 Ndipo ndidzakucurukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzacuruka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzacitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

12 Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israyeli; adzakhala nawe dziko lao lao, ndipo udzakhala colowa cao osafetsanso ana ao.

13 Atero Ambuye Yehova, Popeza akuti nawe, Dzikowe ukudya anthu, nuyesa anthu ako afedwa;

14 cifukwa cace sudzadyanso anthu, kapena kuyesanso amtundu wako afedwa, ati Ambuye Yehova.

15 Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzaseozanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova.

Za kukonzekanso kwa Israyeli

16 Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,

17 Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israyeli anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi macitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga cidetso ca mkazi wooloka.

18 M'mwemo ndinawatsanulira ukali wanga, cifukwa ca mwazi anautsanulira padziko, ndi cifukwa ca mafano analidetsa dziko nao;

19 ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m'maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa macitidwe ao ndinawaweruza.

20 Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, naturuka m'dziko mwace.

21 Koma ndinawaleka cifukwa ca dzina langa loyera, limene a nyumba ya Israyeli adalidetsa pakati pa amitundu, kumene adarakako,

22 Cifukwa cace nena kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Sindicicita ici cifukwa ca inu, nyumba ya Israyeli, koma cifukwa ca dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako.

23 Ndipo ndidzazindikiritsa dzina langa lalikuru kuti liri loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, limene inu munaliipsa pakati pao; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ati Ambuye Yehova, pozindikiridwa Ine woyera mwa inu pamaso pao.

24 Pakuti ndidzakutengani kukuturutsani kwa amitundu, ndi kukusokolotsani m'maiko onse, ndi kubwera nanu m'dziko lanu.

25 Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukucotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu onse.

26 Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzacotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.

27 Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwacita.

28 Ndipo mudzakhala m'dziko ndinapatsa makolo anulo, ndipo mudzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu.

29 Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumcurukitsa, osaikiranso inu njala.

30 Ndipo ndidzacurukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m'munda, kuti musalandirenso citonzo ca njala mwa amitundu.

31 Pamenepo mudzakumbukila njira zanu zoipa, ndi zocita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, cifukwa ca mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.

32 Dziwani kuti sindicita ici cifukwa ca inu, ati Ambuye Yehova; citani manyazi, dodomani, cifukwa ca njira zanu, nyumba ya Israyeli inu.

33 Atero Ambuye Yehova, Tsiku loti ndikuyeretsani kukucotserani mphulupulu zanu zonse, ndidzakhalitsa anthu m'midzimo; ndi pamabwinja padzamangidwa.

34 Ndi dziko lacipululu lidzalimidwa, cinkana linali lacipululu pamaso pa onse opitako.

35 Ndipo adzati, Dziko ili lacipululu lasanduka ngati munda wa Edene, ndi midzi yamabwinja, ndi yacipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m'mwemo.

36 Pamenepo amitundu otsala pozungulira panu adzadziwa kuti Ine Yehova ndamanga malo opasuka, ndi kubzala pamene panali cipululu; Ine Yehova ndanena ndidzacita.

37 Atero Ambuye Yehova, Ici comwe adzandipempha a nyumba ya Israyeli ndiwacitire ici, ndidzawacurukitsira anthu ngati nkhosa.

38 Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa madyerero ace oikika, momwemo midzi yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.