1 Caka ca makumi awiri ndi zisanu ca undende wathu, poyamba caka, tsiku lakhumi lamwezi, caka cakhumi ndi zinai atakantha mudziwo, tsiku lomwelo, dzanja la Mulungu linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.
2 M'masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m'dziko la Israyeli, nandikhalitsa pa phiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mudzi kumwela,
3 Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ace ngati amkuwa, ndi cingwe cabwazi m'dzanja lace, ndi bango loyesa nalo, naima kucipata iye.
4 Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israyeli zonse uziona.
5 Ndipo taonani, panali linga kunja kwace kwa nyumba ya kacisi poizinga, ndi m'dzanja lace la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uli wonse mkono kudza cikhato; ndipo anayesa cimangidweco kucindikira kwace bango limodzi, ndi msinkhu wace bango limodzi.
6 Pamenepo anafika ku cipata coloza kum'mawa, nakwera pa makwerero ace; ndipo anayesa ciundo ca cipata, bango limodzi kucindikira kwace; ndico ciundo coyamba, bango limodzi.
7 Ndi cipinda ca alonda, conse nca bango limodzi m'litali mwace, ndi bango limodzi kupingasa kwace, ndi pakati pa zipinda za alonda mikono isanu, ndi ciundo ca cipata ku mbali ya ku khonde la kucipata m'katimo, bango limodzi.
8 Anayesanso khonde la kucipata ku mbali ya kukacisi, bango limodzi.
9 Pamenepo anayesa khonde la kucipata mikono isanu ndi itatu, ndi mphuthu zace mikono iwiri; ndi khonde la kucipata linaloza kukacisi.
10 Ndi zipinda za alonda za ku cipata ca kum'mawa ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, cakuno ndi cauko.
11 Ndipo anayesa kupingasa kwa cipata pakhoma pace mikono khumi, ndi utali wace wa cipata mikono khumi ndi itatu;
12 ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi cakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi cauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi cakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi cauko.
13 Ndipo anayesa cipata kuyambira ku tsindwi la cipinda ca alonda cimodzi, kufikira ku tsindwi la cinzace, kupingasa kwace ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana.
14 Anamanganso nsaaamira za mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi bwalo la pakati pa cipata lidafikira kunsanamira.
15 Ndipo kuyambira pa khomo lolowera la cipata kufikira khomo la khonde la cipata m'katimo ndiko mikono makumi asanu.
16 Ndipo panali mazenera a made okhazikika pazipinda ndi m'makhoma a pakati pao, m'kati mwa cipata pozungulira ponse; momwemonso pazidundumwa; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m'katimo, pa nsanamirazo panali akanjedza.
17 Pamenepo analowa nane ku bwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.
18 Ndipo moyalidwamo munali pa mbali ya zipata molingana ndi utali wace wa zipata, ndimo moyalidwa mwamunsi.
19 Pamenepo anayesa kupingasa kwace kuyambira pakhomo pace pacipata cakunsi, kufikira kumaso kwace kwa bwalo la m'kati kunja kwace, mikono zana kum'mawa, ndi kumpoto.
20 Ndi cipata ca bwalo lakunja coloza kumpoto anaciyesa m'litali mwace, ndi kupingasa kwace.
21 Ndi zipinda zace ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, ndi makhoma a pakati pace; ndi zidundumwa zace zinali monga mwa muyeso wa cipata coyambaco, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.
22 Ndi mazenera ace, ndi zidundumwa zace, ndi akanjedza ace, anali monga mwa muyeso wa cipata coloza kum'mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi zidundumwa zace zinali pakhomo.
23 Ndipo panali cipata ca bwalo lam'kati, copenyana ndi cipata cinzace cakunja kumpoto, ndi ca kum'mawa; ndipo anayesa kuyambira kucipata kufikira kucipata mikono zana.
24 Ndipo ananditsogolera kumka kumwela, ndipo taonani, panali cipata kumwela, nayesa makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi.
25 Ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo, monga mazenera ena aja, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.
26 Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi zidundumwa zace kumaso kwace; ndi pa nsanamira zace cakuno ndi cauko panali akanjedza.
27 Ndipo panali cipata ca bwalo lam'kati cakulozakumwela, nayesa kuyambira kucipata kufikira kucipata kumwela mikono zana.
28 Pamenepo analowa nane pa cipata ca kumwela m'bwalo lam'kati, nayesa cipata ca kumwera, monga mwa miyeso yomweyi;
29 ndi zipinda zace, ndi makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo; m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.
30 Ndipo panali zidundumwa pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi awiri mphambu isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu.
31 Ndi zidundumwa zace zinaloza ku bwalo lakunja, ndi pa nsanamira zace panali akanjedza, ndi pokwererapo panali makwerero asanu ndi atatu.
32 Ndipo analowa ndine m'bwalo lam'kati kuloza kum'mawa, nayesa cipata ca kum'mawa monga mwa miyeso yomweyi;
33 ndi zipindazace, ndi makhoma a pakati pace, Indi zikundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.
34 Ndi zidundumwa zace zinaloza ku bwalo lakunja; ndi pa nsanamira zace panali akanjedza cakuno ndi cauko; ndipo pokwerera pace panali makwerero asanu ndi atatu.
35 Pamenepo anabwera nane ku cipata ca kumpoto, naciyesa monga mwa miyeso yomweyi;
36 zipinda zace, makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace; ndimo munali mazenera m'menemo pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.
37 Ndi nsanamira zace zinaloza ku bwalo lakunja; ndi pa nsanamira zace panali akanjedza cakuno ndi cauko; ndipo pokwerera pace panali makwerero asanu ndi atatu.
38 Ndipo pa nsanamira za pazipata panali kanyumba ndi citseko cace; pamenepo anatsuka nsembe vopsereza.
39 Ndipo m'khonde la pacipata munali magome awiri cakuno, ndi magome awiri cauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula.
40 Ndi ku mbali yina ya khonde kunja, pakukwerera polowera pa cipata ca kumpoto, kunali magome awiri, ndi ku mbali inzace ya kucipata kunali magome awiri.
41 Magome anai cakuno, ndi magome anai cauko, ku mbali ya cipata; magome asanu ndi atatu, amene anapherapo nsembe.
42 Ndipo panali magome anai a nsembe yopsereza a miyala yosema, m'litali mwace mkono ndi nusu, kupingasa kwace mkono ndi nusu, msinkhu wace mkono umodzi; pamenepo adafoika zipangizo zimene anaphera nazo nsembe yopsereza ndi nsembe yophera.
43 Ndi ziciri zangowe, cikhato m'litali mwace, zinamangika m'katimo pozungulirapo; ndi pamagome panali nyama ya nsembe.
44 Ndi kunja kwa cipata ca m'kati kunali tinyumba ta oyimba m'bwalo lam'kati, ku mbali ya cipata ca kumpoto; ndipo tinaloza kumwela, kena ku mbali ya cipata ca kum'mawa kanaloza kumpoto.
45 Ndipo anati kwa ine, Kanyumba aka koloza kumwela nka ansembe odikira kacisi.
46 Ndi kanyumba koloza kumpoto nka ansembe odikira guwa la nsembe, ndiwo ana a Zadoki amene ayandikira kwa Yehova mwa ana a Levi, kumtumikira Iye.
47 Ndipo anayesa bwalolo mikono zana m'litali mwace, ndi mikono zana kupingasa kwace, lamphwamphwa; ndi guwa la nsembe linali kukhomo kwa nyumba.
48 Pamenepo anadza nane ku khonde la kacisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu cakuno, ndi mikono isanu cauko; ndi kupingasa kwa cipata, mikono itatu cakuno, ndi mikono itatu cauko.
49 M'litali mwace mwa khonde mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono khumi ndi umodzi; ndipo panali makwerero khumi okwerera kumeneko; ndipo panali zoimiritsa pa nsanamirazo, imodzi cakuno, ndi imodzi cauko.