1 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, nenera motsutsana naye Gogi, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Gogi, iwe mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;
2 ndipo ndidzakutembenuza, ndi kukutsogolera, ndi kukweza iwe ucoke ku malekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe ku mapiri a Israyeli;
3 ndipo ndidzakantha uta wako kuucotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mibvi yako ku dzanja lako lamanja.
4 Udzagwa pa mapiri a Israyeli, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zirombo za kuthengo, akuyese cakudya.
5 Udzagwa kuthengo koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova.
6 Ndipo ndidzatumizira moto Magogi, ndi iwo okhala mosatekeseka m'zisumbu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7 Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israyeli, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israyeli.
8 Taonani, cikudza, cidzacitika, ati Ambuye Yehova, ndilo tsiku ndanenalo.
9 Ndipo iwo okhala m'midzi ya Israyeli adzaturuka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zocinjiriza, mauta, ndi mibvi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;
10 osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova.
11 Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ndidzapatsa Gogi manda m'Israyeli, cigwa ca opitawo kum'mawa kwa nyanja; ndipo lidzaletsa opitawo, ndipo adzaika komweko Gogi ndi unyinji wace wonse, nadzacicha, Cigwa ca unyinji wa Gogi.
12 Ndi a nyumba ya Israyeli adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko.
13 Inde anthu onse a m'dziko adzawaika, nadzamveka nako tsiku lakulemekezedwa Ine, ati Ambuye Yehova.
14 Ndipo adzasankha anthu akupita-pitabe m'dziko, ndi pamodzi ndi opitapitawo anthu akuika mafupa otsala pamtunda, kuliyeretsa; pakutha miyezi isanu ndi iwiri adzapwaira.
15 Ndipo opitapitawo adzapitapita m'dziko, ndipo winaakaona pfupa la munthu aikepo cizindikilo, mpaka oikawo aliika m'cigwa ca unyinji wa Gogi.
16 Ndipo dzina la mudzi lidzakhala Hamona. Momwemo adzayeretsa dziko.
17 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse za kuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani ku mbali zonse, kudza ku nsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikuru pa mapiri a Israyeli, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi.
18 Mudzadya nyama ya amphamvu, ndi kumwa mwazi wa akalonga a padziko, wa nkhosa zamphongo, wa ana a nkhosa, ndi wa mbuzi, ndi wa ng'ombe, zonsezi zonenepa za ku Basana.
19 Ndipo mudzadya zonona mpaka mudzakhuta, ndi kumwa mwazi mpaka mudzaledzera za nsembe yanga ndakupherani.
20 Ndipo podyera panga mudzakhuta akavalo, ndi magareta, ndi anthu amphamvu, ndi anthu onse a nkhondo, ati Ambuye Yehova.
21 Ndipo ndidzaika ulemerero wanga mwa amitundu; ndi amitundu onse adzaona ciweruzo canga ndacicita, ndi dzanja langa limene ndinawaikira.
22 Ndipo nyumba ya Israyeli idzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, kuyambira tsiku ilo ndi m'tsogolomo.
23 Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israyeli idalowa undende cifukwa ca mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.
24 Ndinacita nao monga mwa kudetsedwa kwao, ndi monga mwa kulakwa kwao, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.
25 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsopano ndidzabweza undende wa Yakobo, ndi kucitira cifundo nyumba yonse ya Israyeli, ndipo ndidzacitira dzina langa loyera nsanje.
26 Ndipo adzasenza manyazi ao, ndi zolakwa zao zonse, zimene anandilakwira nazo, pokhala mosatekeseka iwo m'dziko lao, opanda wina wakuwaopsa;
27 nditabwera nao kucoka kwa mitundu ya anthu, nditawasokolotsa m'maiko a adani ao, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa iwo pamaso pa amitundu ambiri.
28 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, popeza ndinalola atengedwe ndende kumka kwa amitundu, koma ndinawasonkhanitsanso akhale m'dziko lao, osasiyakonso mmodzi yense wa iwowa.
29 Ndipo sindidzawabisiranso nkhope yanga, popeza ndatsanulira mzimu wanga pa nyumba ya Israyeli, ati Ambuye Yehova.