1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, Dziwitsa Yerusalemu zonyansa zace, nuziti,
3 Atero Ambuye Yehova kwa Yerusalemu, Ciyambi cako ndi kubadwa kwako ndiko ku dziko la Akanani; atate wako anali M-amori, ndi mai wako Mhiti.
4 Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadula ncofu yako, sanakuyeretsa ndi kukusambitsa ndi madzi, sanakuthira mcere konse, kapena kukukulunga m'nsaru ai.
5 Panalibe diso linakucitira cifundo, kukucitira cimodzi conse ca izi, kucitira iwe nsoni; koma unatayidwa kuyere; pakuti ananyansidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwake,
6 Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikubvimvinizika m'mwazi wako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako, Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.
7 Ndinakucurukitsa ngati mphundu za kumunda; ndipo unathululuka ndi kukula kufikira wakongola nkhope, maere ako anamera, ndi tsitsi lako linamera; koma unali wamarisece ndi wausiwa.
8 Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakupfunda copfunda canga, ndi kuphimba umarisece wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.
9 Ndipo ndinakusambitsa ndi madzi, inde ndinakutsuka kukucotsera mwazi wako, ndi kukudzoza mafuta.
10 Ndinakubvekanso ndi nsaru zopikapika, ndi kukubveka nsapato za cikopa ca katumbu; ndinakuzenenga nsaru yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsaru yasilika.
11 Ndinakukometseranso ndi zokometsera, ndi kuika zigwinjiri m'manja mwako, ndi unyolo m'khosi mwako.
12 Momwemo ndinaika cipini m'mphuno mwako, ndi maperere m'makutu mwako, ndi korona wokongola pamutu pako.
13 Ndipo unadzikometsera ndi golidi, ndi siliva, ndi cobvala cako ndi bafuta ndi silika ndi yopikapika; unadya ufa wosalala, ndi uci, ndi mafuta; ndipo unali wokongola woposa ndithu, ndipo unapindula-pindula kufikira unasanduka ufumu.
14 Ndi mbiri yako inabuka mwa amitundu cifukwa ca kukongola kwako; pakuti ndiko kwangwiro, mwa ulemerero wanga ndinauika pa iwe, ati Ambuye Yehova.
15 Koma unatama kukongola kwako, ndi kucita zacigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu ali yense wopitapo; unali wace.
16 Ndipo unatengako zobvala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawanga mawanga, ndi kucitapo cigololo; zotere sizinayenera kufika kapena kucitika.
17 Unatenganso zokometsera zako zokoma za golidi wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kucita nao cigololo.
18 Unatenganso zobvala zako za nsaru yopikapika, ndi kuwabveka nazo, unaikanso mafuta anga ndi cofukiza canga pamaso pao.
19 Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uci, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zicite pfungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova.
20 Unatenganso ana ako amuna ndi akazi amene unandibalirawo, ndi kuwapereka nsembe awathe. Zigololo zako zidacepa kodi,
21 kuti unawapha ana anga ndi kuwapereka, pakuwapititsa pamoto?
22 Ndipo pa zonyansa zako zonse ndi zigololo zako sunakumbukila masiku a ubwana wako, mujaunakhala wamarisece ndi wausiwa, wobvimvinizika m'mwazi wako.
23 Ndipo kudacitika utatha zoipa zako zonse, (tsoka iwe, tsoka, ati Ambuye Yehova)
24 unadzimangira nyumba yacimphuli, unadzimangiranso ciunda m'makwalala ali onse.
25 Unamanga ciunda cako pa mphambano ziri zonse, ndipo unanyansitsa kukongola kwako, ndi kutukula mapazi ako kwa yense wopitako, ndi kucurukitsa cigololo cako.
26 Wacitanso cigololo ndi Aaigupto oyandikizana nawe, akulu thupi, ndi kucurukitsa cigololo cako kuutsa mkwiyo wanga.
27 Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kucepsa gawo lako la cakudya, ndi kukupereka ku cifuniro ca iwo akudana nawe, kwa ana akazi a Afilisti akucita manyazi ndi njira yako yoipa.
28 Unacitanso cigololo ndi Aasuri, pakuti unakhala wosakoledwa, inde unacita cigololo nao, koma sunakoledwa.
29 Unacurukitsanso cigololo cako m'dziko la Kanani, mpaka dziko la Akasidi, koma sunakoledwa naconso.
30 Ha! mtima wako ngwofoka, ati Ambuye Yehova, pakucita iwe izi zonse, ndizo nchito za mkazi wacigololo wouma m'maso.
31 Pakumanga nyumba yako yacimphuli pa mphambano ziri zonse, ndi pomanga ciunda cako m'makwalala ali onse, sunakhala ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.
32 Ndiwe mkazi wokwatibwa wocita cigololo, wolandira alendo m'malo mwa mwamuna wace.
33 Anthu amaninkha akazi onse acigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kucokera ku mbali zonse, kuti acite nawe cigololo.
34 M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'cigololo cako; pakuti palibe wokutsata kucita nawe cigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.
35 Cifukwa cace, wacigololo iwe, tamvera mau a Yehova:
36 Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nubvundukuka umarisece wako mwa cigololo cako ndi mabwenzi ako, ndi cifukwa ca mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawa patsa;
37 cifukwa cace taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwabvundukulira umarisece wako, kuti aone umarisece wako wonse.
38 Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi acigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.
39 Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yacimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakubvula zobvala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamarisece ndi wausiwa.
40 Ndipo adzamemezera iwe msonkhano, nadzakuponya miyala, ndi kukupyoza ndi malupanga ao.
41 Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto, nadzakuweruza pamaso pa akazi ambiri; ndipo ndidzakuleketsa kucita cigololo, ndipo sudzalipiranso mphotho yacigololo.
42 M'mwemo ukali wanga udzakhuta nawe, ndi nsanje yanga idzakucokera, ndipo ndidzakhala cete wosakwiyanso.
43 Popeza sunakumbukila masiku a ubwana wako, koma wandibvuta nazo zonsezi, cifukwa cace taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzacita coipa ici coonjezerapo pa zonyansa zako zonse.
44 Taona, ali yense wonena miyambi adzakunenera mwambi uwu, wakuti, Monga mace momwemo mwana wace.
45 Iwe ndiwe mwana wa mako wonyansidwa naye mwamuna wace ndi ana ace, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Mhiti, ndi atate wako ndiye M-amori.
46 Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala ku dzanja lako lamanzere, iye ndi ana ace akazi; ndi mng'ono wako wokhala ku dzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ace akazi.
47 Koma sunayenda m'njira zao, kapena kucita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kubvunda kwako, m'njira zako zonse.
48 Pali ine, ati Ambuye Yehova, Sodomu mng'ono wako sanacita, iye kapena ana ace akazi, monga umo unacitira iwe ndi ana ako akazi.
49 Taona, mphulupulu ya mng'onowako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kucuruka kwa cakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ace; ndipo sanalimbitsa dzanja la wosauka ndi wosowa.
50 Ndipo anadzikuza, nacita conyansa pamaso panga; cifukwa cace ndinawacotsa pakuciona.
51 Ngakhale Samariya sanacita theka la zocimwa zako, koma unacurukitsa zonyansa zako kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazicita.
52 Usenzenso manyazi ako, iwe wakuweruza abale ako mwa zocimwa zako unazicita monyansa koposa iwowa; iwo akuposa iwe m'cilungamo cao, nawenso ucite manyazi nusenze manyazi ako, popeza waika abale ako olungama.
53 Ndipo ndidzabweza undende wao, undende wa Sodomu ndi ana ace, ndi undende wa Samariya ndi ana ace, ndi undede wa andende ako pakati pao;
54 kuti usenze manyazi ako, ndi kuti ucite manyazi cifukwa ca zonse unazicita pakuwatonthoza.
55 Ndipo abale ako Sodomu ndi ana ace adzabwerera umo unakhalira kale; ndi iwe ndi ana ako mudzabwerera umo munakhalira kale.
56 Ndipo sunakamba za mbale wako Sodomu pakamwa pako tsiku la kudzikuza kwako;
57 cisanabvundukuke coipa cako monga nthawi ya citonzo ca ana akazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana akazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse.
58 Wasenza coipa cako ndi zonyansa zako, ati Yehova.
59 Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzacita ndi iwe monga umo unacitira; popeza wapepula lumbiro ndi kutyola pangano.
60 Koma ndidzakumbukila Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.
61 Pamenepo udzakumbukila njira zako ndi kucita manyazi, pakulandira abale ako akuru ndi ang'ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako akazi, angakhale sali a pangano lako.
62 Pakuti ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova;
63 kuti uzikumbukila ndi kucita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, cifukwa ca manyazi ako, pamene ndikufafanima zonse unazicita, ati Ambuye Yehova.