1 Ndipo iwe, takwezera akalonga a Israyeli nyimbo ya maliro,
2 uziti, Mai wako ndi ciani? Mkango waukazi unabwanthama mwa mikango, unalera ana ace pakati pa misona.
3 Ndipo unalera mmodzi wa ana ace, iye nasanduka msona, unaphunzira kugwira nyama, unalusira anthu.
4 Mitundu ya anthu idamva mbiri yace, unagwidwa m'mbuna mwao; ndipo anadza nao ndi zokowera ku dziko la Aigupto.
5 Pakuona tsono waukaziwo, kuti unalindirira, ndi kuti ciyembekezo cace cidatha, unatenga wina wa ana ace, numsandutsa msona.
6 Ndipo unayendayenda pakati pa mikango, nukhala msona, nuphunzira kugwira nyama, nulusira anthu.
7 Ndipo unadziwa amasiye ao, nupasula midzi yao, ndipo dziko ndi kudzala kwace linasanduka labwinja, cifukwa ca phokoso la kubangula kwace.
8 Pamenepo mitundu ya anthu inadzipereka kuukola kucokera ku maiko a ku mbali zonse, niuphimba ndi ukonde wao, nugwidwa uwu m'mbuna mwao.
9 Nauika m'citatanga ndi zokowera, nadza nao kwa mfumu ya ku Babulo; anaulonga m'malinga, kuti mau ace asamvekenso pa mapiri a Israyeli.
10 Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, cifukwa ca madzi ambiri.
11 Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zacifumu, za ocita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, nizinaoneka m'kusomphoka kwao pakati pa nthambi zace zambiri.
12 Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum'mawa, inaumitsa zipatso zace, ndodo zace zolimba zinatyoka ndi kuuma, moto unazitha.
13 Ndipo tsopano waokedwa m'cipululu m'dziko louma ndi la ludzu.
14 Unaturukanso moto ku ndodo za ku nthambi zace, unatha zipatso zace; m'mwemo ulibe ndodo yolimba ikhale ndodo yacifumu ya kucita ufumu. Iyi ndi nyimbo idzakhala nyimbo ya maliro.