1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, ndiye mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;
3 nunenere motsutsana naye, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe, Gogi iwe, mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;
4 ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'cibwano mwako ndi zokowera, ndi kukuturutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo obvala mokwanira onsewo, msonkhano waukuru ndi zikopa zocinjiriza, onsewo ogwira, bwino malupanga;
5 Perisiya, Kusi, ndi Puti pamodzi nao, onsewo ndi cikopa ndi cisoti cacitsulo;
6 Gomeri ndi magulu ace onse, nyumba ya Togarima, ku malekezero a kumpoto, ndi magulu ace onse, mitundu yambiri pamodzi ndi iwe.
7 Ukonzekeretu, Inde udzikonzeretu, iwe ndi msonkhano wako wonse unakusonkhanira, nukhale iwe mtsogoleri wao.
8 Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m'dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituruke m'mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israyeli, amene adakhala acipululu cikhalire; koma liturutsidwa m'mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo.
9 Ndipo udzakwera udzadza ngati mkuntho, udzanga mtambo kuphimba dziko, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.
10 Atero Ambuye Yehova, Kudzacitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira ciwembu coipa,
11 nudzati, Ndidzakwera kumka ku dziko la midzi yopanda malinga, ndidzamka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mipingiridzo, kapena zitseko;
12 kulanda ndi kufunkha zao, kubweza dzanja lako liononge mopasuka muli anthu tsopano, liononge mtundu wa anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoweta ndi cuma, okhala pakati pa dziko.
13 Seba, ndi Dedani, ndi amalonda a Tarisi, ndi misona yace yonse ya mikango adzati kwa iwe, Wadza kodi kudzafunkha? wasonkhanitsa kodi msonkhano wako kulanda, kucoka nazo siliva ndi golidi, kucoka nazo zoweta ndi cuma, kulanda zankhondo zambiri?
14 Cifukwa cace nenera, wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israyeli, sudzacidziwa kodi?
15 Ndipo udzaturuka m'malo mwako m'malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe, onsewo apakavalo, msonkhano waukuru ndi nkhondo yaikuru;
16 ndipo udzakwerera anthu anga Israyeli ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzacitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao.
17 Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israyeli, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?
18 Ndipo kudzacitika tsiku ilo, tsiku loti Gogi adzadza kulimbana ndi dziko la Israyeli, ati Ambuye Yehova, ukali wanga udzakwera m'mphuno mwanga.
19 Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukuru m'dziko la Israyeli;
20 motero kuti nsomba za m'nyanja, ndi mbalame za m'mlengalenga, ndi nyama za kuthengo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, ndi anthu onse akukhala padziko, zidzanjenjemera pamaso panga; ndi mapiri adzagwetsedwa, ndi potsetsereka padzagumuka, ndi makoma onse adzagwa pansi.
21 Ndipo ndidzamuitanira lupanga ku mapiri anga onse, ati Ambuye Yehova, munthu ali yense lupanga lace lidzaombana nalo la mbale wace.
22 Ndipo ndidzalimbana naye ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzambvumbitsira iye, ndi magulu ace, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mbvumbi waukuru, ndi matalala akuru, moto ndi sulfure.
23 Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziwika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.