1 Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Turo ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Onyo, watyoka uwu udali cipata ca mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;
3 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Turo, ndidzakukweretsera amitundu, monga nyanja iutsa mafunde ace.
4 Ndipo adzagumula malinga a Turo, ndi kugwetsa nsanja zace; inde ndidzausesa pfumbi lace, ndi kuuyesa pathanthwe poyera.
5 Udzakhala poyanika khokapakati pa nyanja, pakuti Ine ndacinena, ati Ambuye Yehova; ndipo udzakhala cofunkha ca amitundu.
6 Ndi ana ace akazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Turo Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mfumu ya mafumu, yocokera kumpoto ndi akavalo, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri.
8 Ana ako akazi adzawapha kumunda ndi lupanga; ndipo adzakumangira nsanja, ndi kukuundira mtumbira, ndi kukuimikira cikopa.
9 Nadzaikira malinga ako zogumulira, nadzagwetsa nsanja zako ndi zida zace.
10 Papeza acuruka akavalo ace, pfumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magareta, palowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m'mudzi popasukira linga lace.
11 Ndi ziboda za akavalo ace iye adzapondaponda m'makwalala ako onse; adzapha anthu ako ndi lupanga; ndi zoimiritsa za mphamvu yako zidzagwa pansi.
12 Ndipo adzalanda cuma cako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi pfumbi lako, m'madzi.
13 Ndipo ndidzaleketsa phokoso la nyimbo zako, ndi kulira kwa mazeze ako sikudzamvekanso.
14 Ndipo ndidzakuyesa pathanthwe poyera; udzakhala poyanika khoka, sadzakumanganso; pakuti Ine Yehova ndacinena, ati Ambuye Yehova.
15 Atero Ambuye Yehova kwa Turo, Zisumbu sizidzagwedezeka nanga pomveka kugwa kwako, pabuula olasidwa, pakucitika kuphako pakati pako?
16 Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yacifumu yao, nadzabvula zobvala zao zopikapika, nadzabvala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kukudabwa.
17 Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pakhala pa anthu a panyanja, mudzi womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo!
18 Pamenepo zisumbu zidzanjenjemera tsiku la kugwa kwako, inde zisumbu za kunyanja zidzatenga nkhawa pa kucokera kwako.
19 Pakuti atero Ambuye Yehova, Pamene ndikusandutsa mudzi wapasuka, ngati midzi yosakhalamo anthu, ndi kukukweretsera nyanja, nadzakumiza madzi akuru;
20 pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa ku malo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,
21 ndidzakuika woopsa; ndipo sudzaonekanso, cinkana akufunafuna sudzapezekanso konse, ati Ambuye Yehova.