Ezekieli 13 BL92

1 Ndipo mau a Yehova anandidzera ine, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israyeli onenerawo, nuziti nao onenera za m'mtima mwao mwao, Tamverani mau a Yehova.

3 Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu wao wao, cinkana sanaona kanthu.

4 Aneneri ako, Israyeli, akhala ngati nkhandwe m'mapululu.

5 Simunakwera kuima mopasuka, kapena kumanganso linga la nyumba ya Israyeli, kuima kunkhondo tsiku la Yehova.

6 Iwo aona zopanda pace, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatuma, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.

7 Simunaona masomphenya opanda pace kodi? simunanena ula wabodza kodi? pakunena inu, Atero Yehova; cinkana sindinanena?

8 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pace, ndi kuona mabodza, cifukwa cace taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.

9 Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pace, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israyeli, kapena kulowa m'dziko la Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova,

10 Popeza, inde popeza asokeretsa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere; ndipo anthu akamanga linga, aneneriwo alimata ndi dothi losapondeka;

11 uziti nao olimata ndi dothi losapondeka, kuti lidzagwa, lidzabvumbidwa ndi mvula yaikuru; ndi inu, matalala akuru, mudzagwa; ndi mkuntho udzalithithimula.

12 Ndipo taonani, litagwa linga, sadzanena nanu kodi, Liri kuti dothi munalimata nalo?

13 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho m'ukali wanga; ndipo lidzabvumbidwa ndi mvula yaikuru mu mkwiyo wanga, ndi matalala akuru adzalitha m'ukali wanga.

14 M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ace agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pace; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

15 M'mwemo ndidzakwaniritsa ukali wanga pa lingalo, ndi pa iwo analimata ndi dothi losapondeka, ndipo ndidzati kwa inu, Lingalo palibe, ndi olimata palibe,

16 ndiwo aneneri a Israyeli akunenera za Yerusalemu, nauonera masomphenya a mtendere, pamene palibe mtendere, ati Ambuye Yehova.

Mau akutsutsa aneneri akazi onama

17 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, uziika nkhope yako itsutsane nao ana akazi a anthu ako, akunenera za m'mtima mwao, nunenere cowatsutsa,

18 nuziti, Atero Ambuye Yehova, Tsoka akazi osoka zophimbira mfundo zonse za dzanja, ndi iwo okonza zokuta mitu za misinkhu iri yonse, kuti asake miyoyo! Kodi musaka miyoyo ya anthu anga ndi kudzisungira miyoyo yanu?

19 Ndipo mundidetsa mwa anthu anga kulandirapo barele wodzala manja, ndi zidutsu za mkate, kuipha miyoyo yosayenera kufa, ndi kusunga miyoyo yosayenera kukhala ndi moyo, ndi kunena mabodza kwa anthu anga omvera bodza.

20 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taonani, nditsutsana nazo zophimbira zanu, zimene musaka nazo miyoyo komweko, kululuza; ndipo ndidzazikwatula m'manja mwanu, ndi kuimasula, ndiyo miyoyo muisaka kululuza.

21 Zokuta mitu zanu zomwe ndidzazing'amba, ndi kulanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo sadzakhalanso m'mphamvu mwanu kusakidwa; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

22 Popeza mwamvetsa cisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetsa cisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yace yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;

23 cifukwa cace simudzaonanso zopanda pace, kapena kupenda; koma ndidzalanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.