Ezekieli 42 BL92

Kukonzekanso kwa Kacisi: zipinda zopatulika

1 Pamenepo anaturuka nane kumka ku bwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane ku nyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto.

2 Cakuno ca m'litali mwace mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwace mikono makumi asanu.

3 Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzace losanjikika paciwiri.

4 Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwace mikono khumi m'kati mwace, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto.

5 Ndipo zipinda zapamwamba zinacepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, cifukwa cace zinacepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda.

6 Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; cifukwa cace zam'mwambazo zinacepa koposa zakunsi ndi zapakati kuyambira pansi.

7 Ndipo linga linali kunialo, loli'ngana ndi nyumba yazipinda, kuloza ku bwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwace munali mikono makumi asanu.

8 Pakuti kupingasa kwace kwa nyumba yazipinda inali m'bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza ku khomo la Kacisi inali mikono zana limodzi.

9 Ndipo pansi pa zipinda izi panali polowera mbali ya kum'mawa, poloweramo kucoka ku bwalo lakunja.

10 M'kucindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, cakuno ca mpatawo, cakuno ca nyumba, panali nyumba yazipinda.

11 Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe a njira ya ku nyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m'litali mwace, momwemonso kupingasa kwace; ndi m'maturukiro mwace monse munali monga mwa macitidwe a inzace, ndi monga mwa makomo a inzace.

12 Ndi monga mwa makomo a zipinda za kumwela panali khomo polekeza njira, ndiyo njira yokhudzana ndi linga la kum'mawa polowamo.

13 Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwela, ziri cakuno ca mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulikitsa; kumeneko aziika zopatulikitsa, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula; pakuti malowo ndi opatulika.

14 Atalowa ansembe asaturukenso m'malo opatulika kumka ku bwalo lakunja, koma komweko aziika zobvala zao zimene atumikira nazo; pakuti ziri zopatulika; ndipo abvale zobvala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.

15 Atatha tsono kuyesa nyumba ya m'katimo, anaturuka nane njira ya cipata coloza kum'mawa, nayesa bwalo pozungulira pace.

16 Anayesa mbali ya kum'mawa ndi bango loyesera, mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera, pozungulira pace.

17 Anayesa mbali ya kumpoto mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera, pozungulira pace.

18 Anayesa mbali ya kumwela mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera,

19 Anatembenukira ku mbali ya kumadzulo, nayesa mabango mazana asanu ndi bango loyesera.

20 Analiyesa mbali zace zinai, linali nalo linga pozungulira pace, utali wace mazana asanu, citando cace mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zawamba.