1 Pamenepo anafika kwa ine akulu ena a Israyeli nakhala pansi pamaso panga.
2 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
3 Wobadwa ndi munthu iwe, anthu awa anautsa mafano ao mumtima mwao, naimika cokhumudwitsa ca mphulupulu yao pamaso pao; ndifunsidwe nao konse kodi?
4 Cifukwa cace ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Ali yense wa nyumba ya Israyeli wakuutsa mafano ace mumtima mwace, naimika cokhumudwitsa ca mphulupulu yace pamaso pace, nadza kwa mneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ace aunyinji;
5 kuti ndigwire nyumba ya Israyeli mumtima mwao; popeza onsewo asanduka alendo ndi Ine mwa mafano ao.
6 Cifukwa cace uziti kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Bwerani, lekani mafano anu, tembenuzani nkhope zanu kuzisiya zonyansa zanu zonse.
7 Pakuti ali yense wa nyumba ya Israyeli, kapena wa alendo ogonera m'Israyeli, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ace m'mtima mwace, naimika cokhumudwitsa ca mphulupulu yace pamaso pace, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;
8 ndipo ndidzaikira munthu uyu nkhope yanga imtsutse, ndi kumuyesa codabwitsa, ndi cizindikilo, ndi mwambi, ndi kumsadza pakati pa anthu anga; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
9 Ndipo akaceteka mneneriyo, nakanena mau, Ine Yehova ndamceta mneneri uja; ndipo ndidzamtambasulira dzanja langa, ndi kumuononga pakati pa anthu anga Israyeli.
10 Ndipo adzasenza mphulupulu yao, mphulupulu ya mneneri idzanga mphulupulu ya uja wamfunsira;
11 kuti nyumba ya Israyeli isasocerenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova.
12 Ndipo anandidzera mau a Yehova akuti,
13 Likandicimwira dziko ndi kucita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulityolera mcirikizo wace, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,
14 cinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Danieli, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa cilungamo cao, ati Ambuye Yehova.
15 Ndikapititsa zirombo zoipa pakati pa dziko, nizipulula ana, kuti likhale lacipululu losapitako munthu cifukwa ca zirombo,
16 cinkana anthu omwewo atatu akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lacipululu.
17 Kapena ndikadza pa dziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati pa dziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama;
18 cinkana anthu atatuwo akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; koma iwo akadapulumuka okha.
19 Kapena ndikatumizira dzikolo mliri, ndi kulitsanulira ukali wanga ndi mwazi, kulidulira munthu ndi nyama;
20 cinkana Nowa, Danieli, ndi Yobu, akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi cilungamo cao.
21 Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zirombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?
22 Koma onani mudzatsala opulumuka m'mwemo amene adzaturutsidwa, ndiwo ana amuna ndi akazi; taonani, adzaturuka kudza kwa inu; ndipo mudzaona njira zao, ndi zocita zao; mudzatonthozedwanso pa zoipa ndazitengera pa Yerusalemu, inde pa zonse ndazitengerapo.
23 Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zocita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazicita kopanda cifukwa zonse ndinazicita momwemo, ati Ambuye Yehova.