Ezekieli 23 BL92

Ohola ndi Oholiba acigololowo

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, panali akazi awiri, mai wao ndi mmodzi;

3 ndipo anacita cigololo iwo m'Aigupto, anacita cigololo m'ubwana wao; pomwepo anthu anasindikiza maere ao, pomweponso anakhudza nsonga za maere za unamwali wao.

4 Ndipo maina ao ndiwo Ohola wamkuru, ndi Oholiba mng'ono wace; nakhala anga, nabala ana amuna ndi akazi. Ndipo maina ao, Samariya ndiye Ohola, ndi Yerusalemu ndiye Oholiba.

5 Koma Ohola anacita cigololo pamene anali wanga, anaumirira mabwenzi ace Aasuri oyandikizana naye;

6 obvala cibakuwa, ziwanga, ndi akazembe, onsewo anyamata ofunika, anthu oyenda pa akavalo.

7 Ndipo anacita nao zigololo zace, ndiwo anthu osankhika a ku Asuri onsewo, ndipo ali onse anawaumirira anadziipsa nao mafano ao.

8 Sanalekanso zigololo zace zocokera ku Aigupto, pakuti anagona naye m'unamwali wace, nakhudza maere a unamwali wace, namtsanulira cigololo cao.

9 Cifukwa cace ndampereka m'dzanja la mabwenzi ace, m'dzanja la Aasuri amene anawaumirira.

10 Iwowa anabvula umarisece wace, anatenga ana ace amuna ndi akazi, namupha iyeyu ndi lupanga; ndi dzina lace linamveka mwa akazi atamcitira maweruzo.

11 Pamene mng'ono wace Oholiba anaciona, anabvunda ndi kuumirira kwace koposa iyeyo; ndi zigololo zace zidaposa zigololo za mkuru wace.

12 Anaumirira Aasuri, ziwanga, ndi akazembe oyandikizana naye, obvala zangwiro, anthu oyenda pa akavalo, onsewo anyamata ofunika.

13 Ndipo ndinamuona kuti anadetsedwa, onse awiri adatenga njira yomweyi.

14 Ndipo anaonjeza zigololo zace, naona amuna olembedwa pakhoma, zithunzithunzi za Akasidi olembedwa ndi kundwe;

15 omangira malamba m'cuuno mwao, ndi nduwira zazikuru zonika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babulo, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.

16 Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga ku dziko la Akasidi.

17 Namdzera a ku Babulo ku kama wa cikondi, namdetsa ndi cigololo cao, iyenso anadetsedwa nao; atatero moyo wace unafukidwa nao.

18 M'mwemo iye anaulula cigololo cace, nabvula umarisece wace; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkuru wace.

19 Koma anacurukitsa zigololo zace, nakumbukila masiku a ubwana wace, muja anacita cigololo m'dziko la Aigupto.

20 Ndipo anaumirira amuna ao amene nyama yao ikunga ya aburu, ndi kutentha kwao ngati kutentha kwa akavalo.

21 Momwemo wautsanso coipa ca ubwana wako, pakukhudza Aaigupto nsonga za maere ako, cifukwa ca maere a ubwana wako.

22 Cifukwa cace, Oholiba, atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakuutsira mabwenzi ako amene moyo wako wakufidwa nao, ndi kukufikitsira iwowa pozungulira ponse atsutsane nawe,

23 a ku Babulo, ndi Akasidi, Pekodi, ndi Sowa, ndi Kowa, ndi Aasuri onse pamodzi nao, anyamata ofunika, ziwanga ndi akazembe onsewo, akalonga ndi mandoda onsewo, oyenda ndi akavalo.

24 Ndipo adzakudzera ndi zida, magareta a nkhondo, ndi magareta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zocinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao.

25 Ndipo ndidzakuikira nsanje yanga, nadzakucitira mwaukali, iwowa adzakudula mphuno ndi makutu; ndi otsiriza ako adzagwa ndi lupanga, adzakucotsera ana ako amuna ndi akazi, ndi otsirizira ako adzatha ndi moto.

26 Adzakubvulanso zobvala zako, ndi kukucotsera zokometsera zako zokongola.

27 Motero ndidzakuleketsera coipa cako, ndi cigololo cako cocokera m'dziko la Aigupto; ndipo sudzazikwezeranso maso ako, kapena kukumbukiranso Aigupto,

28 Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakupereka m'dzanja la iwo amene uwada, m'dzanja la iwo amene moyo wako ufukidwa nao;

29 ndipo adzacita nawe mwaudani, nadzalanda zonse udazigwirira nchito, nadzakusiya wamarisece ndi wausiwa; ndi umarisece wa zigololo zako udzabvulidwa, dama lako ndi zigololo zako zomwe.

30 Izi adzakucitira cifukwa watsata amitundu, ndi kucita nao cigololo, popezanso wadetsedwa ndi mafano ao.

31 Wayenda m'njira ya mkuru wako, cifukwa cace ndidzapereka cikho cace m'dzanja lako.

32 Atero Ambuye Yehova, M'cikho ca mkuru wako udzamweramo ndico cacikuru ngati mcenje; adzakuseka pwepwete, nadzakunyoza muli zambiri m'menemo.

33 Udzadzala ndi kuledzera ndi cisoni, ndi cikho codabwitsa ndi ca cipasuko, ndi cikho ca mkuru wako Samariya.

34 Udzamwa ici ndi kugugudiza, ndi kuceceta-ceceta zibade zace, ndi kung'amba maere ako; pakuti ndacinena, ati Ambuye Yehova.

35 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso coipa cako ndi zigololo zako.

36 Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? uwafotokozere tsono zonyansa zao.

37 Pakuti anacita cigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anacita cigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao amuna amene anandibalira, kuti athedwe.

38 Anandicitiranso ici, anadetsa malo anga opatulika tsiku lomwelo naipsa masabata anga;

39 pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m'malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m'kati mwa nyumba yanga.

40 Ndiponso munatuma kuitana anthu ocokera kutali, ndiwo munawatumira mthenga; ndipo taona, anadza amenewo unasamba, cifukwa ca iwo unapaka maso ako mankhwala, ndi kubvala zokometsera;

41 ndipo unakhala pa kama waulemu, pali gome lokonzekeratu patsogolo pace; pamenepo unaika cofukiza conga ndi mafuta anga.

42 Ndipo phokoso lalikuru lidaleka pomwepo, ndipo pamodzi ndi anthu wamba anabwera nao alodzera ocokera kucipululu, naika makoza m'manja mwa awiriwo, ndi akorona okongola pamitu pao.

43 Pamenepo ndinati za uyu anakalamba nazo zigololo, Tsopano iwo adzacita zigololo naye, ndi iyenso nao.

44 Ndipo analowa kwa iye monga umo amalowera kwa mkazi wacigololo, motero analowa kwa Ohola ndi Oholiba akazi oipawo.

45 Ndipo anthu olungama adzawaweruza monga mwa maweruzo a acigololo, ndi maweruzo a akazi okhetsa mwazi; pakuti ndiwo acigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi.

46 Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzawakweretsera msonkhano wa anthu, ndi kuwapereka awazunze, ndi kulanda cuma cao.

47 Ndi msonkhanowo udzawaponya miyala, ndi kuwatha ndi malupanga ao, adzawapha ana ao amuna ndi akazi, ndi kutentha nyumba zao ndi moto.

48 Momwemo ndidzaleketsa dama m'dzikomo, kuti alangizidwe akazi onse kusacita monga mwa dama lanu.

49 Ndipo adzakubwezerani dama lanu, nimudzasenza macimo a mafano anu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.