1 Anandidzeranso mau a Yehova caka cacisanu ndi cinai, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, ndi kuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, Udzilembere dzina la tsiku lomwe lino, mfumu ya ku Babulo wayandikira Yerusalemu tsiku lomwe lino.
3 Ndipo uphere nyumba yopandukayo fanizo, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tereka mphika; uutereke, nuthire madzi m'menemo.
4 Longamo pamodzi ziwalo zace, ziwalo zonse zokoma, mwendo wathako ndi wamwamba; uudzaze ndi mafupa osankhika.
5 Tengako coweta cosankhika, nuikire mafupa mulu wa nkhuni pansi; ubwadamuke, ndi mafupa ace omwe uwaphike m'mwemo.
6 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, mphika m'mene muli dzimbiri, losaucokera dzimbiri lace; ucotsemo ciwalo ciwalo; sanaugwera maere.
7 Pakuti mwazi wace uli m'kati mwace anauika pathanthwe poyera, sanautsanulira panthaka kuukwirira ndi pfumbi.
8 Pofuna kuutsa ukali, ndi kubwezera cilango, ndaika mwazi wace pathanthwe poyera, kuti usakwiririke.
9 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, ndidzakulitsa mulu wa nkhuni.
10 Zicuruke nkhuni, kuleza moto, nyama ipse, uwiritse msuzi wace, ubwadamuke, ndi mafupa ace atibuke.
11 Pamenepo uukhazike pa makara ace opanda kanthu m'menemo, kuti utenthe, nuyake mkuwa wace; ndi kuti codetsa cace cisungunuke m'mwemo, kuti dzimbiri lace lithe.
12 Nchito ya mphika ndi yolemetsa, koma dzimbiri lace lalikuru siliucokera, dzimbiri lace liyenera kumoto.
13 M'codetsa cako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukucotsera codetsa cako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.
14 Ine Yehova ndacinena, cidzacitika; ndipo ndidzacicita, sindidzamasula, kapena kulekerera, kapena kuwaleka, monga mwa njira zako, ndi monga umo unacitira adzakuweruza iwe, ati Ambuye Yehova.
15 Mau a Yehova anandidzeranso, akuti,
16 Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikucotsera cokonda maso ako ndi cikomo, koma usamve cisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi.
17 Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire cilemba, nubvale nsapato ku mapazi ako, usaphimbe milomo yako, kapena kudya mkate wa anthu.
18 Ndipo nditalankhula ndi anthu m'mawa, madzulo ace mkazi wanga anamwalira; ndi m'mawa mwace ndinacita monga anandilamulira.
19 Nanena nane anthu, Simudzatiuza kodi zitani nafe izi muzicita?
20 Ndipo ndinanena nao, Anandidzera mau a Yehova, akuti,
21 Nena ndi nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, cokonda m'maso mwanu, cimene moyo wanu ali naco cifundo; ndipo ana anu amuna ndi akazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.
22 Ndipo mudzacita monga umo ndacitira ine, osaphimba milomo yanu, kapena kudya mkate wa anthu.
23 Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu ku mapazi anu, simudzacita cisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzace.
24 Momwemo Ezekieli adzakhala kwa inu cizindikilo; umo monse anacitira iye mudzacita ndinu; cikadza ici mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
25 Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwacotsera mphamvu yao, cimwemwe cao copambana, cowakonda m'maso mwao, ndi cokhumbitsa mtima wao, ana ao amuna ndi akazi,
26 kuti tsiku lomwelo wopulumukayo adzakudzera, kukumvetsa m'makutu mwako?
27 Tsiku lomwelo pakamwa pako padzatsegukira wopulumukayo; mudzalankhula osakhalanso cete, momwemo udzawakhalira cizindikilo; ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.