Ezekieli 3 BL92

1 Ndipo ananena nane, Wobadwa ndi munthu iwe, Idya cimene wacipeza; idya mpukutu uwu, numuke ndi kunena ndi nyumba ya Israyeli.

2 Pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndipo anandidyetsa mpukutuwo.

3 Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uci.

4 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Muka, nufike kwa nyumba ya Israyeli, nunene nao mau anga.

5 Pakuti sutumizidwa kwa anthu a cinenedwe cosamveka ndi cobvuta, koma kwa nyumba ya Israyeli;

6 si kwa mitundu yambiri ya anthu a cinenedwe cosamveka ndi cobvuta, amene sukhoza kudziwitsa cinenedwe cao. Zedi ndikakutumiza kwa iwowa adzamvera iwe.

7 Koma nyumba ya Israyeli siidzakumvera, pakuti siifuna kundimvera Ine; pakuti nyumba yonse ya Israyeli ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima.

8 Taona ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zao; ndalimbitsanso mutu wako utsutsane nayo mitu yao.

9 Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pao; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.

10 Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako.

11 Numuke, nufike kwa andende kwa ana a anthu a mtundu wako, nunene nao ndi kuwauza, Atero Yehova Mulungu, ngakhale akamva kapena akaleka kumva.

12 Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukuru, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwace.

13 Ndipo ndinamva mkokomo wa mapiko a zamoyozo pakukhudzana, ndi mlikiti wa njingazo m'mbali mwa izo, ndilo phokoso la mkokomo waukuru.

14 M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kucoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa,

15 Ndipo ndinafika kwa andende ku Telabibu, okhala kumtsinje Kebara, ndiko kwao; ndipo ndinakhalako woda bwa pakati pao masiku asanu ndi awiri.

Mlonda wa Israyeli

16 Ndipo kunali atatha masiku asanu ndi awiri, mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,

17 Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israyeli, m'mwemo mvera mau oturuka m'kamwa mwanga, nundicenjezere iwo.

18 Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamcenjeza, wosanena kumcenjeza woipayo aleke njira yace yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yace; koma mwazi wace ndidzaufuna pa dzanja lako.

19 Koma ukacenjeza woipa, osabwerera iye kuleka coipa cace kapena njira yace yoipa, adzafa mu mphulupulu yace; koma iwe walanditsamoyo wako.

20 Momwemonso akabwerera wolungama kuleka cilungamo cace, ndi kucita cosalungama, ndipo ndikamuikira comkhumudwitsa, adzafa; popeza sunamcenjeza, adzafa m'cimo lace, ndi zolungama zace adazicita sizidzakumbukika; koma mwazi wace ndidzaufuna pa dzanja lako.

21 Koma ukamcenjeza wolungamayo, kuti asacimwe wolungamayo, ndipo sacimwa, adzakhala ndi moyo ndithu, popeza anacenjezedwa; ndipo iwe walanditsa moyo wako.

22 Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, turuka kumka kucidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.

23 Ndipo ndinauka ndi kuturuka kumka kucidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona ku mtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi.

24 Pamenepo unandilowa mzimu ndi kundiimika ndikhale ciriri; ndipo analankhula ndi ine, nanena nane, Muka, katsekedwe m'nyumba mwako.

25 Koma iwe wobadwa ndi munthu, taona, adzakuikira iwe zingwe zolimba, nadzakumanga nazo, ndipo sudzaturuka pakati pao;

26 ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako ku malakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.

27 Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako, nudzanena nao, Atero Yehova Mulungu. Wakumvera amvere, wasafuna kumvera akhale; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.