Ezekieli 20 BL92

Macimo a Aisrayeli citurukire iwo m'dziko la Aigupto

1 Ndipo kunali caka cacisanu ndi ciwiri, mwezi wacisanu; tsiku lakhumi la mwezi, anadza akulu ena a Israyeli kufunsira kwa Yehova, nakhala pansi iwowa pamaso panga.

2 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

3 Wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi akulu a Israyeli, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova.

4 Udzawaweruza kodi, wobadwa ndi munthu iwe? udzawaweruza? uwadziwitse zonyansa za makolo ao,

5 nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija ndinamsankha Israyeli, ndi kukwezera mbeu ya nyumba ya Yakobo dzanja langa, ndi kudzidziwitsa kwa iwo m'dziko la Aigupto, pakuwakwezera dzanja langa, ndi kuti, Ine ndine Yehova Mulungu wanu;

6 tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwaturutsa m'dziko la Aigupto, kumka nao ku dziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uci, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;

7 ndipo ndinanena nao, Ali yense ataye zonyansa za pamaso pace, nimusadzidetsa ndi mafano a Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

8 Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataya yense zonyansa pamaso pace, sanaleka mafano a Aigupto; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Aigupto.

9 Koma ndinacicita cifukwa ca dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwaturutsa m'dziko la Aigupto.

10 Momwemo ndinaturuka nao m'dziko la Aigupto, ndi kulowa nao kucipululu.

11 Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo.

12 Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale cizindikilo pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.

13 Koma nyumba ya Israyeli inapaodukira Ine m'cipululu, sanayenda m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene, munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'cipululu kuwatha.

14 Koma ndinacicita cifukwa ca dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawaturutsa pamaso pao.

15 Ndipo ndinawakwezeranso dzanja langa m'cipululu, kusawalowetsa m'dzikolo ndidawapatsa, moyenda mkaka ndi uci, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;

16 popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.

17 Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawatha onse m'cipululu.

18 Ndipo ndinati kwa ana ao m'cipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;

19 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, muziyenda m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwacita;

20 muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala cizindikilo pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

21 Koma anawo anapandukira Ine, sanayenda m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwacita, amene munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'cipululu.

22 Koma ndinabweza dzanja langa ndi kucicita, cifukwa ca dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawaturutsa pamaso pao. Ndinawakwezeranso dzanja langa m'cipululu,

23 kuti ndidzawabalalitsa mwa amitundu, ndi kuwamwaza m'maiko;

24 popeza sanacita maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao.

25 Momwemonso ndinawapatsa malemba amene sanali abwino, ndi maweruzo osakhala nao ndi moyo;

26 ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.

27 Cifukwa cace wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israyeli, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa icinso atate anu anandicitira mwano pakundilakwira Ine.

28 Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya citunda ciri conse cacitali, ndi mtengo uli wonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, napetekapo nsembe zao zondiputa, aponso anacita pfungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.

29 Pamenepo ndinanena nao, Msanje wotani uwu mumapitako? Momwemo dzina lace lichedwa Msanje, mpaka lero lino.

30 Cifukwa cace uziti kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Mudzidetsa kodi monga umo anacitira makolo anu? mucita cigololo kodi kutsata zonyansa zao?

31 ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israyeli? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;

32 ndi ici cimauka mumtima mwanu sicidzacitika, umo mukuti, Tidzakhala ngati amitundu, ngati mabanja a m'maiko, kutumikira mtengo ndi mwala.

Mulungu adzabweza Israyeli kucokera kobalalikidwa iwo

33 Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa, ndidzakhala mfumu yanu.

34 Ndipo ndidzakuturutsani mwa mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani m'maiko munabalalikamo ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa.

35 Ndipo ndidzalowa nanu m'cipululu ca mitundu ya anthu, ndi kukuweruzani komweko popenyana maso.

36 Monga ndinaweruza makolo anu m'cipululu ca dziko la Aigupto, momwemo ndidzaweruza inu, ati Ambuye Yehova.

37 Ndipo ndidzakupititsani pansi pa ndodo ya mbusa ndi kukulowetsani m'cimango ca cipangano;

38 ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawaturutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israyeli; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

39 Ndipo inu, nyumba ya Israyeli, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ace, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvera Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.

40 Pakuti pa phiri langa lopatulika, pa phiri lothubvuka la Israyeli, ati Ambuye Yehova, pomwepo onse a nyumba ya Israyeli, onsewo adzanditumikira Ine m'dzikomo; pomwepo ndidzawalandira, ndi pomwepo ndidzafuna nsembe zanu zokweza, ndi zoyamba za msonkho wanu, pamodzi ndi zopatulika zanu zonse.

41 Ngati pfungo lokoma ndidzakulandirani pakukuturutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukucotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.

42 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakukulowetsani Ine m'dzil ko la Israyeli, m'dzikoli ndinalikwezera dzanja langa kulipereka kwa makolo anu.

43 Ndi pomwepo mudzakumbukila njira zanu, ndi zonse mudazicita ndi kudzidetsa nazo, ndipo mudzakhala onyansa pamaso pa inu nokha, cifukwa ca zoipa zanu zonse mudazicita.

44 M'mwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova nditacita nanu cifukwa ca dzina langa, si monga mwa njira zanu zoipa, kapena monga mwa macitidwe anu obvunda, nyumba ya Israyeli inu, ati Ambuye Yehova.

45 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

46 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango ya kuthengo la kumwera kwa Yuda;

47 nuziti kwa nkhalango ya kumwera kwa Yuda, Tamvera mau a Yehova, Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzayatsa moto mwa iwe, udzanyeketsa mtengo uli wonse wauwisi mwa iwe, ndi mtengo uli wonse wouma; malawi amoto sadzazimika, ndi nkhope zonse kuyambira kumwera kufikira kumpoto zidzapsa nao.

48 Ndi anthu onse adzaona kuti Ine Yehova ndinauyatsa, sudzazimika.

49 Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! anandinena, Wonena mafanizo uyu.