Ezekieli 43 BL92

Kukonzekanso kwa Kacisi: ulemerero wa Mulungu

1 Pamenepo anamuka nane ku cipata coloza kum'mawa,

2 ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ace ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wace.

3 Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona ku mtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.

4 Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa m'kacisi kudzera njira ya cipata coloza kum'mawa.

5 Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane ku bwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu unadzaza kacisi.

6 Ndipo ndinamva wina alikulankhula nane ali m'kacisi, naima nane munthu.

7 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wacifumu wanga, mpoponda ku mapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israyeli kosatha; ndi nyumba ya Israyeli siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa cigololo cao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,

8 ndi kuika ciundo cao pafupi pa ciundo canga, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazicita; cifukwa cace ndinawatha mu mkwiyo wanga.

9 Ataye tsono cigololo cao ndi mitembo ya mafumu ao kutali kwa Ine, ndipo ndidzakhala pakati pao kosatha.

10 Wabadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israyeli kacisiyu, kuti acite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wace.

11 Ndipo ngati akacita manyazi nazo zonse anazicita, uwadziwitse maonekedwe a kacisiyu, ndi muyeso wace, ndi poturukira pace, ndi polowera pace, ndi malongosoledwe ace onse, ndi malemba ace onse, ngakhale maonekedwe ace onse, ndi malamulo ace onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ace onse, ndi malemba ace onse, nawacite.

12 Lamulo la kacisi ndi ili: pamwamba pa phiri malire ace onse pozungulira pace azikhala opatulikitsa. Taonani, limeneli ndi lamulo la kacisi.

13 Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi cikhato), tsinde lace likhale mkono, ndi kupingasa kwace mkono, ndi mkuzi wace m'mphepete mwace pozungulira pace kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.

14 Ndi kuyambira kunsi kwace kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwace mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikuru mikono inai; ndi kupingasa kwace mkono.

15 Ndi guwa lapamwamba mikono inai; ndi pamoto pa guwa padzaturuka nyanga zinai.

16 Ndi pamoto pa guwa, m'litali mwace mikono khumi ndi iwiri, ndi kupingasa kwace khumi ndi iwiri, lampwamphwa mbali zace zinai.

17 Ndi phaka, m'litali mwace mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwace mikono khumi ndi inai ku mbali zace zinai; ndi mkuzi wace pozungulira pace mkono wa nusu, ndi tsinde lace mkono pozungulira pace, ndi makwerero ace aloza kum'mawa.

18 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, atero Ambuye Yehova, Malemba a guwa la nsembe, tsiku lakulimanga, kuperekapo nsembe zopsereza, ndi kuwazapo mwazi, ndi awa;

19 Upatse ansembe Alevi, a mbeu ya Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwana wa ng'ombe, akhale wa nsembe yaucimo.

20 Nutengeko mwazi wace, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pa ngondya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wace pozungulira; motero uliyeretse ndi kulicitira cotetezera.

21 Utengenso ng'ombe ya nsembe yaucimo, aipsereze pa malo oikika a kacisi kunja kwa malo opatulika.

22 Ndipo tsiku laciwiri upereke tonde wopanda cirema, akhale nsembe yaucimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo.

23 Utatha kuliyeretsa upereke mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta yopanda cirema.

24 Ndipo ubwere nazo kwa Yehova, ndi ansembe athirepo mcere, ndi kuzipereka nsembe yopsereza ya Yehova.

25 Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yaucimo; akonzerenso mwana wa ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda cirema.

26 Masiku asanu ndi awiri acite cotetezera guwali ndi kuliyeretsa, momwemo alipatule.

27 Ndipo atatsiriza masiku, kudzacitika tsiku lacisanu ndi citatu ndi m'tsogolo, ansembe azicita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika pa guwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova.