Ezekieli 28 BL92

Aneneratu za kulangidwa kwa mfumu ya ku Turo

1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2 Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Turo, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,

3 taona, ndiwe wanzeru woposa Danieli, palibe cinsinsi angakubisire;

4 mwa nzeru zako ndi luntha lako wadzionerera cuma, wadzionereranso golidi ndi siliva mwa cuma cako;

5 mwa nzeru zako zazikuru ndi kugulana malonda kwako wacurukitsa cuma cako, ndi mtima wako wadzikuza cifukwa ca cuma cako;

6 cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu;

7 cifukwa cace taona, ndidzakufikitsira alendo oopsa a mitundu ya anthu, iwo adzasololera malupanga ao nzeru zako zokongola, nadzaipsa kunyezimira kwako.

8 Adzakutsitsira kumanda, nudzafa mafedwe a ophedwa m'kati mwa nyanja.

9 Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.

10 Udzafa mafedwe a osadulidwa ndi dzanja la alendo, pakuti ndacinena, ati Ambuye Yehova.

Nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Turo

11 Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,

12 Wobadwa ndi munthu iwe, kweza nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Turo, nuziti kwa iye, Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi cizindikilo, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro.

13 Unali m'Edene, munda wa Mulungu, mwala uli wonse wa mtengo wace unali copfunda cako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golidi; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.

14 Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali pa phiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.

15 Unali wangwiro m'njira zako cilengedwere iwe, mpaka cinapezeka mwa iwe cosalungama.

16 Mwa kucuruka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi ciwawa, ndipo unacimwa; cifukwa cace ndinakukankha kukucotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukucotsa pakati pa miyala yamoto.

17 Unadzikuza mtima cifukwa ca kukongola kwako, waipsa nzeru zako; cifukwa ca kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye.

18 Mwa mphulupulu zako zocuruka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; cifukwa cace ndaturutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.

19 Onse akudziwa iwe mwa mitundu ya anthu adzadabwa nawe; wasanduka coopsa, ndipo sudzakhalanso konse.

Za kulangidwa kwa Zidoni

20 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

21 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Zidoni, nuunenere;

22 uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Zidoni, ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakucita Ine maweruzo mwa uwu, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa uwu.

23 Pakuti ndidzatumiza mliri ndi mwazi ilowe m'makwalala ace, ndi olasidwa adzagwa m'kati mwace ndi lupanga lougwera pozungulira ponse; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

24 Ndipo nyumba ya Israyeli siidzakhalanso nayo mitungwi yolasa, kapena minga yaululu ya ali yense wakuizinga ndi kuipeputsa; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

25 Atero Ambuye Yehova, Pakusonkhanitsa nyumba ya Israyeli mwa mitundu ya anthu anabalalikamo, ndidzazindikirika Woyera mwa iwowa, pamaso pa amitundu; ndipo adzakhala m'dziko mwao mwao ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga.

26 Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kunka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.