1 Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane ku cipata ca kum'mawa ca nyumba ya Yehova coloza kum'mawa; ndipo taonani, pa citseko ca cipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu.
2 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mudzi muno;
3 ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mudzi uwu ndi mphika, ife ndife nyama.
4 Cifukwa cace uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe.
5 Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo ananti kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israyeli, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m'mtima mwanu.
6 Mwacurukitsa ophedwa anu m'mudzi muno, mwadzazanso makwalala ace ndi ophedwawo.
7 Cifukwa cace atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwace, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzaturutsidwa m'kati mwace.
8 Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu.
9 Ndipo ndidzakuturutsani m'kati mwace, ndi kukuperekani m'manja a alendo, ndi kucita maweruzo pakati panu.
10 Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani ku malire a Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
11 Mudzi uno sudzakhala mphika wanu, ndi inu simudzakhala nyama m'kati mwace, ndidzakuweruzirani ku malire a Israyeli;
12 ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayenda m'malemba anga, kapena kucita maweruzo anga, koma mwacita monga mwa maweruzo a amitundu okhala pozungulira panu.
13 Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kupfuula ndi mau akuru, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu! mudzatsiriza kodi otsala a Israyeli?
14 Ndipo mau a Yehova anandidzera kuti,
15 Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako amuna a cibale cako, ndi nyumba yonse ya Israyeli, yonseyi ndiwo amene okhala m'Yerusalemu ananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale colowa cathu;
16 cifukwa cace uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawacotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m'maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi ku maiko adafikako.
17 Cifukwa cace uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani ku mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani mucoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israyeli.
18 Ndipo adzafikako, nadzacotsako zonyansa zace zonse, ndi zace zonse zakuipitsamo.
19 Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawacotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;
20 kuti ayende m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwacita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.
21 Koma iwo amene mtima wao unatsata mtima wa zonyansa zao, ndi zoipitsitsa zao, ndidzawabwezera njira yao pamtu pao, ati Yehova Mulungu.
22 Pamenepo akerubi anatambasula mapiko ao, ndi njinga zinali pa mbali pao; ndi ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unali pamwamba pao.
23 Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kucoka pakati pa mudzi, nuima pa phiri la kum'mawa kwa mudzi.
24 Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu ku dziko la Akasidi, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandicokera, nakwera.
25 Pamenepo ndinanena ndi andendewo zonse zija adandionetsa Yehova.