1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, Nena ndi ana a anthu a mtundu wako, uziti nao, Ndikafikitsira dziko liri lonse lupanga, nakatenga eni dziko munthu wa pakati pao, nakamuika awadikirire,
3 nakaona iye lupanga lirikudzera dziko, nakaomba lipenga ndi kucenjeza anthu;
4 ndipo wina, kumva adamva mau a lipenga, koma osalabadira, likadza lupanga, nilimcotsa, wadziphetsa ndi mtima wace.
5 Anamva mau a lipenga, osawalabadira, wadziphetsa ndi mtima wace; akadalabadira, akadalanditsa moyo wace.
6 Koma mlonda akaona lupanga likudza, osaomba lipenga, osacenjeza anthu, nilidza lupanga, nilicotsa mwa iwo; munthu atengedwadi m'mphulupulu zace, koma mwazi wace ndidzaufunsa pa dzanja la mlonda.
7 Iwe tsono, wobadwa ndi munthu, ndakuika mlonda wa nyumba ya Israyeli, m'mwemo imva mau a pakamwa panga, nundicenjezere iwo.
8 Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumcenjeza woipayo aleke njira yace, woipa uyo adzafa m'mphulupulu yace, koma mwazi wace ndidzaufunsa pa dzanja lako.
9 Koma ukacenjeza woipa za njira yace, aileke; koma iye osaileka njira yace, adzafa m'mphulupulu mwace iye, koma iwe walanditsa moyo wako.
10 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nena kwa nyumba ya Israyeli, Mumatero inu ndi kuti, Zolakwa zathu ndi zocimwa zathu zitikhalira, ndipo ticita nazo liwondewonde, tidzakhala ndi moyo bwanji?
11 Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yace, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israyeli?
12 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, unene ndi ana a anthu amtundu wako, Colungama ca wolungama sicidzamlanditsa tsiku la kulakwa kwace, ndi kunena za coipa ca woipa, sadzagwa naco tsiku lakubwerera iye kuleka coipa cace; ndi munthu wolungama sadzakhoza kukhala ndi moyo ndi cilungamo cace tsiku lakucimwa iye.
13 Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama cilungamo cace, akacita cosalungama, sizikumbukika zolungama zace ziri zonse; koma m'cosalungama cace anacicita momwemo adzafa.
14 Ndipo ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu: koma akabwerera iye kuleka cimo lace, nakacita coyenera ndi colungama;
15 woipayo akabweza cikole, nakabweza ico anacilanda mwacifwamba, nakayenda m'malemba a moyo wosacita cosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
16 Zoipa zace ziri zonse anazicita sizidzakumbukika zimtsutse, anacita coyenera ndi colungama; adzakhala ndi moyo ndithu.
17 Koma ana a anthu a mtundu wako akuti, Njira ya Ambuye siiyenera; koma iwowa njira yao siiyenera.
18 Akabwerera wolungama kuleka cilungamo cace, nakacita cosalungama, adzafa m'mwemo.
19 Ndipo woipa akabwerera kuleka coipa cace, nakacita coyenera ndi colungama, adzakhala ndi moyo nazo.
20 Koma munati, Njira ya Ambuye siiyenera. Nyumba ya Israyeli inu, ndidzakuweruzani, yense monga mwa njira zace.
21 Ndipo kunali caka cakhumi ndi ciwiri ca undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lacisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mudzi.
22 Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m'mawa, m'mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula.
23 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
24 Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala ku mabwinja a dziko la Israyeli anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko colowa cace; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife colowa cathu.
25 Cifukwa cace unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu ku mafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko colowa canu?
26 Mumatama lupanga lanu, mumacita conyansa, mumaipsa yense mkazi wa mnansi wace; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko colowa canu?
27 Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zirombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.
28 Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lacipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yace yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israyeli adzakhala acipululu, osapitako munthu.
29 Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, posanduliza Ine dziko likhale lacipululu ndi lodabwitsa, cifukwa ca zonyansa zao zonse anazicita.
30 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, ana a anthu a mtundu wako anena za iwe ku makoma ndi ku makomo a nyumba zao, nanenana yense ndi mbale wace, ndi kuti, Tiyeni tikamve mau ofuma kwa Yehova.
31 Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawacita; pakuti pakamwa pao anena mwacikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.
32 Ndipo taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yacikondi ya woyimba bwino, woyimba limba bwino; pakuti akumva mau ako, koma osawacita.
33 Ndipo pakucitika ici, pakuti cifikadi, pamenepo adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.