1 Atero Ambuye Yehova, Pa cipata ca bwalo lam'kati coloza kum'mawa patsekedwe masiku asanu ndi limodzi ogwira nchito; koma tsiku la Sabata patsegulidwe, ndi tsiku lokhala mwezi patsegulidwe.
2 Ndipo kalonga azilowera njira ya ku khonde la cipataco, kunja kwace, naime ku nsanamira ya cipata; ndipo ansembe akonze nsembe yace yopsereza, ndi nsembe zace zoyamika, nalambire iye ku ciundo ca cipata; atatero aturuke; koma pacipata pasatsekedwe mpaka madzulo.
3 Ndipo anthu a m'dziko alambire pa citseko ca cipata ici pamaso pa Yehova pamasabata, ndi pokhala mwezi.
4 Ndipo nsembe yopsereza imene kalonga azipereka kwa Yehova pa Sabata ndiyo ana a nkhosa asanu ndi mmodzi opanda cirema, ndi nkhosa yamphongo yopanda cirema,
5 ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini a wa mafuta wa paefa.
6 Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndi ana a nkhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda cirema;
7 ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa.
8 Ndipo polowa kalonga azilowera njira ya ku khonde la cipata, naturuke njira yomweyo.
9 Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'madyerero oikika, iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumpoto kudzalambira, aturukire njira ya ku cipata ca kumwera; ndi iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumwera, aturukire njira ya ku cipata ca kumpoto; asabwerere njira ya cipata anadzeraco, koma aturukire m'tsogolo mwace.
10 Kalongayo tsono, polowa iwo alowe pakati pao, ndipo poturuka iwo aturukire pamodzi.
11 Ndi pamadyerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.
12 Ndipo kalonga akapereka copereka caufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa cipata coloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yace yopsereza, ndi nsembe zace zoyamika, monga umo amacitira tsiku la Sabata; atatero aturuke; ndipo ataturuka, wina atseke pacipata.
13 Uziperekanso kwa Yehova mwana wa nkhosa wa caka cimodzi akhale nsembe yopsereza wopanda cirema, tsiku ndi tsiku, m'mawa ndi m'mawa, uzimpereka.
14 Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m'mawa ndi m'mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusanganiza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha.
15 Momwemo apereke mwana wa nkhosa, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta, m'mawa ndi m'mawa, nsembe yopsereza kosalekeza.
16 Atero Ambuye Yehova, Kalonga akapatsa mwana wace wina wamwamuna mphatso idzakhala colowa cace, ndico cao cao ca ana ace, colowa cao.
17 Koma akapatsa mphatso yotenga ku colowa cace kwa wina wa anyamata ace, idzakhala yace mpaka caka ca ufulu; pamenepo ibwerere kwa kalonga, koma colowa cace cikhale ca ana ace.
18 Ndipo kalonga asatengeko colowa ca anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko lao lao; apatse ana ace colowa kulemba dziko lace lace, kuti anthu anga asabalalike, yense kucoka m'dziko lace.
19 Pamenepo anapita ndi ine podzera paja pali ku mbali ya cipata kumka ku zipinda zopatulika za ansembe zoloza kumpoto; ndipo taonani, kunali malo cauko kumadzulo.
20 Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yoparamula, ndi nsembe yaucimo; kumenenso azioca mikate ya ufa wa nsembe, kuti asaturuke nazo ku bwalo lakunja ndi kupatulikitsa anthu,
21 Pamenepo anaturukira nane ku bwalo lakunja, nandipititsa ku ngondya zinai za bwaloli; ndipo taonani, m'ngondya monse munali bwalo.
22 M'ngondya zinai za bwalo munali mabwalo ocingika, m'litali mwace mikono makumi anai, kupingasa kwace makumi atatu; awa anai m'ngondyazi analingana muyeso wace.
23 Ndipo panali maguwa pozungulira pace m'menemo, pozungulira pace pa mabwalo anai; ndipo anamanga maguwawo ndi mafuwa pansi pace pozungulirapo.
24 Ndipo anati kwa ine, Izi ndi nyumba zophikiramo, kumene atumiki a kacisi aziphikira nsembe ya anthu.