1 Ndipo kunali caka cacisanu ndi cimodzi, mwezi wacisanu ndi cimodzi, tsiku lacisanu la mweziwo, pokhala ine m'nyumba mwanga, akulu a Yuda omwe analikukhala pamaso panga, dzanja la Yehova Mulungu linandigwera komweko.
2 Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, cifaniziro ca maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kunsi kwace, moto; ndi kuyambira m'cuuno mwace ndi kumwamba kwace, monga maonekedwe a ceza, ngan citsulo cakupsa.
3 Ndipo anatambasula conga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati pa dziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku citseko ca cipata ca bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje locititsa nsanje.
4 Ndipo taonani, pomwepo panali ulemerero wa Mulungu wa lsrayeli, monga mwa maonekedwe ndinawaona ku cidikha cija.
5 Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako ku njira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga ku njira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa cipata ca guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pace.
6 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzicita? zonyansa zazikulu nyumba ya Israyeli irikuzicita kuno, kuti ndicoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.
7 Ndipo anadza nane ku cipata ca kubwalo, ndipo popenya ine, taonani, pobooka palinga.
8 Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, booletsa kulinga; ndipo nditabooletsa palinga, ndinaona khomo.
9 Ndipo anati kwa ine, Lowa, kapenye zonyansa zoipa alikuzicita komweko.
10 M'mwemo ndinalowa ndi kupenya, ndipo taonani, maonekedwe ali onse a zokwawa, ndi zirombo zonyansa, ndi mafano onse a nyumba ya Israyeli, zolembedwa pakhoma pozungulira ponse.
11 Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israyeli, ndi pakati pao panaima Jazaniya mwana wa Safana munthu ali yense ndi mbale yace ya zofukiza m'dzanja lace; ndi pfungo lace la mtambo wa zonunkhira linakwera.
12 Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi cocita akulu a nyumba ya lsrayeli mumdima, ali yense m'cipinda cace ca zifanizo? pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.
13 Anatinso kwa ine, Udzaonanso zonyansa zazikuru zina azicita.
14 Pamenepo anadza nane ku citseko ca cipata ca nyumba ya Yehova coloza kumpoto; ndipo taonani, apo panakhala akazi akulirira Tainuzi.
15 Ndipo anati kwa ine, Waciona ici, wobadwa ndi munthu iwe? udzaonanso zonyansa zazikuru zoposa izi.
16 Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kacisi wa Yehova, pakati pa khonde lace ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kacisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa; napembedza dzuwa kum'mawa.
17 Ndipo anati kwa ine, Waciona ici, wobadwa ndi munthu iwe? Cinthu copepuka ici kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti acite zonyansa azicita kunozi? pakuti anadzaza dziko ndi ciwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.
18 Cifukwa cace Inenso ndidzacita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawacitira cifundo Ine; ndipo cinkana apfuula m'makutu mwanga ndi mau akulu, koma sindidzawamvera ine.