1 Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, nenera, uziti, Atero Ambuye Yehova, Liritsani, Ha, tsikulo
3 Pakuti layandikira tsiku, layandikira tsiku la Yehova, tsiku lamitambo, ndiyo nyengo ya amitundu.
4 Ndi lupanga lidzadzera Aigupto, ndi m'Kusi mudzakhala kuwawa kwakukuru, pakugwa ophedwa m'Aigupto; ndipo adzacotsa aunyinji ace, ndi maziko ace adzagadamuka,
5 Kusi, ndi Puti, ndi Ludi, ndi osokonezeka onse, ndi Kubi, ndi anthu a dziko lopangana nao, adzagwa pamodzi nao ndi lupanga.
6 Atero Yehova, Iwonso ocirikiza Aigupto adzagwa, ndi mphamvu yace yodzikuza idzatsika, kuyambira nsanja ya Sevene adzagwa m'kati mwace ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.
7 Ndipo adzakhala opasuka pakati pa maiko opasuka, ndi midzi yace idzakhala pakati pa midzi yopasuka.
8 Ndipo adzadziwa, kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto m'Aigupto, naonongeka onse akumthandiza.
9 Tsiku ilo mithenga idzaturuka pamaso panga m'zombo kuopsa Akusi osalabadira; ndipo kudzakhala kuwawa kwakukuru pakati pao, monga tsiku la Aigupto, pakuti taona, likudza.
10 Atero Ambuye Yehova, Ndidzaleketsa kusokosera kwa Aigupto ndi dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo.
11 Iye ndi anthu ace pamodzi naye, woopsa amitundu, adzatengedwa aliononge dzikolo, nadzasololera Aigupto malupanga ao, ndi kudzaza dziko ndi ophedwa.
12 Ndipo ndidzaphwetsa mitsinje, ndi kugulira dziko m'dzanja la anthu oipa, ndipo ndidzalisandutsa likhale dziko lopasuka, ndi zonse ziri m'mwemo mwa dzanja la alendo; Ine Yehova ndacinena.
13 Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pace ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wocokera ku Aigupto, ndipo ndidzaopsa dziko la Aigupto.
14 Ndipo ndidzasandutsa Patro labwinja, ndi kuika moto m'Zoani, ndi kukwaniritsa maweruzo m'No.
15 Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika peni peni pa Aigupto, ndi kulikha aunyinji a No.
16 Ndipo ndidzaika moto m'Aigupto; Sini adzamva kuwawa kwakukuru, ndi No adzagawika pakati, ndi Nofu adzaona adani usana.
17 Anyamata a Avene ndi Pibezeti adzagwa ndi lupanga, ndi midziyi idzalowa undende.
18 Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakutyola Ine magoli a Aigupto komweko; ndi mphamvu yace yodzikuza idzalekeka m'menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ace akazi adzalowa undende.
19 Motero ndidzakwaniritsa maweruzo m'Aigupto, ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
20 Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, mwezi woyamba, tsiku lacisanu ndi ciwiri la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
21 Wabadwa ndi munthu iwe, ndatyola dzanja la Parao mfumu ya Aigupto, ndipo taona, silinamangidwa kuti lipole, kulikulunga ndi nsaru, kulilimbitsa ligwire lupanga.
22 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Parao mfumu ya Aigupto, ndidzatyola manja ace, lolimba ndi lotyokalo, ndi kutayitsa lupanga m'dzanja lace.
23 Ndipo ndidzamwaza Aaigupto mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.
24 Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babulo, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lace; koma ndidzatyola manja a Parao, ndipo adzabuula pamaso pace mabuulo a munthu wopyozedwa.
25 Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babulo, koma manja a Parao adzagwa; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuika Ine lupanga langa m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, nalitambasula Iye pa dziko la Aigupto.
26 Ndipo ndidzamwaza Aaigupto mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa mwa amitundu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.