Ezekieli 47 BL92

Masomphenya a madzi oturuka m'Kacisi watsopano

1 Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa ciundo ca nyumba kum'mawa; pakuti khomo lace la nyumba linaloza kum'mawa; ndipo madzi anatsika kucokera pansi pa nyumba, ku mbali ya lamanja lace, kumwela kwa guwa la nsembe.

2 Pamenepo anaturuka nane njira ya ku cipata ca kumpoto, nazungulira nane njira yakunja kumka ku cipata cakunja, njira ya ku cipata coloza kum'mawa; ndipo taonani, panaturuka madzi pa mbali ya kulamanja.

3 Poturuka munthuyu kumka kum'mawa ndi cingwe coyesera m'dzanja lace, anayesa mikono cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'kakolo.

4 Nayesanso cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'maondo. Nayesanso cikwi cimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'cuuno.

5 Atatero anayesanso cikwi cimodzi, ndipo mtsinje wosakhoza kuoloka ine, popeza madzi adakula, madzi osambira, mtsinje wosaoloka munthu.

6 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, waona ici? Nanditenga kundikwezetsa ndi mtsinje.

7 Nditabwera tsono, taonani, pa gombe la mtsinjewo mitengo yambirimbiri tsidya lino ndi lija.

8 Pamenepo anati kwa ine, Madzi awa aturukira ku dera la kum'mawa, natsikira kucidikha, nayenda kunyanja; atathira kunyanja akonzeka madzi ace.

9 Ndipo kudzatero kuti zamoyo zonse zocuruka zidzakhala ndi moyo kuti konse mtsinjewo ufikako, ndi nsomba zidzacuruka kwambiri; pakuti madzi awa anafikako, nakonzeka madzi a m'nyanja; ndipo kuli konse mtsinje ufikako ziri zonse zidzakhala ndi moyo.

10 Ndipo kudzacitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Eneglaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundu mitundu, ngati nsomba za m'nyanja yaikuru, zambirimbiri.

11 Koma pali matope ace ndi zithaphwi zace sipadzakonzeka, paperekedwa pakhale pamcere.

12 Ndipo kumtsinje, kugombe kwace tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uli wonse wa cakudya, osafota tsamba lace, zipatso zace zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ace atumphuka m'malo opatulika; ndi zipatso zace zidzakhala cakudya, ndi tsamba lace lakuciritsa.

Malire a dziko

13 Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale colowa cao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.

14 Ndipo mudzakhala nalo colowa canu wina ndi mnzace yemwe, ndilo limene ndinakwezapo dzanja langa kulipereka kwa makolo anu, ndi dziko ili lidzakugwerani colowa canu.

15 Ndipo malire a dzikoli ndi awa: mbali ya kumpoto, kuyambira ku nyanja yaikuru, kutsata njira ya ku Heteloni, kufikira polowera ku Zedadi;

16 Hamati, Berota, Sibraimu, ndiwo pakati pa malire a Damasiko, ndi malire a Hamati; Hazere Hatikoni ndiwo ku malire a Haurani.

17 Ndi malire ocokera kunyanja ndiwo Hazaremoni, ku malire a Damasiko, ndi kumpoto kulinga kumpoto kuli malire a Hamati, Ndiyo mbali ya kumpoto.

18 Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Gileadi, ndi dziko la Israyeli, ndiwo Yordano; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa.

19 Ndi mbali ya kumwela kuloza kumwela ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meriboti Kadesi, ku mtsinje wa Aigupto, ndi ku nyanja yaikuru. Ndiyo mbali ya kumwela kuloza kumwela.

20 Ndi mbali ya kumadzulo ndiyo nyanja yaikuru, kuyambira malire a kumwela kufikira pandunji polowera ku Hamati. Ndiyo mbali ya kumadzulo.

21 Motero mudzigawire dziko ili monga mwa mafuko a Israyeli.

22 Ndipo kudzacitika kuti muligawe ndi kucita maere, likhale colowa canu, ndi ca alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israyeli, alandire colowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israyeli.

23 Ndipo kudzatero kuti kupfuko kumene mlendo akhalako kumeneko mumpatse colowa cace, ati Ambuye Yehova.