1 Pamenepo anandibweza njira ya ku cipata cakunja ca malo opatulika coloza kum'mawa, koma cinatsekedwa.
2 Ndipo Yehova anati kwa ine, Cipata ici citsekeke, cisatseguke, osalowako munthu; pakuti Yehova Mulungu wa Israyeli walowerapo; cifukwa cace citsekeke.
3 Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe ku njira ya ku khonde la cipata, naturukire njira yomweyi.
4 Atatero anamuka nane njira ya cipata ca kumpoto kukhomo kwa kacisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi.
5 Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m'makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ace onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi maturukidwe ace onse a malo opatulika.
6 Nunene kwa opandukawo, kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Nyumba ya Israyeli inu, Zikukoleni zonyansa zanu zonse;
7 popeza mwalowa nao acilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munatyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.
8 Ndipo simunasunga udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira mokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika.
9 Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m'mtima, wosadulidwa m'thupi, alowe m'malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israyeli.
10 Koma Aleviwo anandicokera kumka kutariwo, posokera Israyeli, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao.
11 Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira ku zipata za kacisi, ndi kutumikira m'kacisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera naime pamaso pao kuwatumikira.
12 Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala cokhumudwitsa ca mphulupulu ca nyumba ya Israyeli, cifukwa cace ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao.
13 Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira nchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga ziri zonse zopatulikitsazo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazicita.
14 Koma ndidzawaika akhale osunga udikiro wa kacisi kwa utumiki wace wonse, ndi zonse zakumacitika m'mwemo.
15 Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israyeli, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;
16 iwowa adzalowa m'malo anga opatulika, nadzayandikira ku gome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga.
17 Ndipo kudzatero, polowa iwo ku zipata za bwalo lam'kati abvale zobvala zabafuta; koma zaubweya asazibvale ponditumikira Ine m'zipata za bwalo la m'kati, ndi m'kacisi.
18 Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m'cuuno mwao; asabvale m'cuuno kanthu kali konse kakucititsa thukuta.
19 Ndipo akaturukira ku bwalo lakunja, ku bwalo lakunja kuti anthu, azibvula zobvala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, nabvale zobvala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.
20 Ndipo asamete mitu yao, kapena asalekerere nzera za tsitsi lao zikule, azingosenga mitu yao.
21 Kungakhale kumwa vinyo, wansembe asamwe polowa ku bwalo la m'katimo.
22 Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asacite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israyeli, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.
23 Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.
24 Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pa madyerero anga onse oikika; napatulikitse masabata anga.
25 Ndipo asayandikire kwa munthu ali yense wakufa, angadzidetse; koma cifukwa ca atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.
26 Ndipo atayeretsedwa amwerengere masiku asanu ndi awiri.
27 Ndipo tsiku loti alowa m'malo opatulika, bwalo lam'kati, kutumikira m'malo opatulika, apereke nsembe yace yaucimo, ati Ambuye Yehova.
28 Ndipo adzakhala naco colowa; Ine ndine colowa cao; musawapatsa colandira cao m'Israyeli; Ine ndine colandira cao.
29 Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula; ndipo ziri zonse zoperekedwa ciperekere m'Israyeli ndi zao.
30 Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu ziri zonse, ndi nsembe za kweza ziri zonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.
31 Ansembe asadyeko kanthu kakufa kokha, kapena kogwidwa ndi cirombo, ngakhale mbalame, kapena nyama.